Categories
EKSODO

EKSODO 10

Chozizwitsa cha 8: Dzombe

1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwaFarao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pao;

2 ndi kuti ufotokozere m’makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita mu Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

3 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;

4 pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m’dziko lako;

5 ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uliwonse wokuphukirani kuthengo;

6 ndipo lidzadzaza m’nyumba zako, ndi m’nyumba za anyamata ako onse, ndi m’nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo padziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao.

7 Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka?

8 Ndipo anawabwereretsa Mose ndi Aroni kwa Farao, nanena nao, Mukani, katumikireni Yehova Mulungu wanu. Koma amene adzapitawo ndiwo yani?

9 Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng’ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova.

10 Ndipo ananena nao, Momwemo, Yehova akhale nanu ngati ndilola inu ndi ana aang’ono anu mumuke; chenjerani pakuti pali choipa pamaso panu.

11 Chotero ai, mukani tsopano, inu amuna aakulu, tumikirani Yehova pakuti ichi muchifuna. Ndipo anawapirikitsa pamaso pa Farao.

12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako padziko la Ejipito, lidze dzombe, kuti likwere padziko la Ejipito, lidye zitsamba zonse za m’dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.

13 Pamenepo Mose analoza ndodo yake padziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum’mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum’mawa inadza nalo dzombe.

14 Ndipo dzombe linakwera padziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.

15 Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m’dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsale chabiriwiri chilichonse, pamitengo kapena pa zitsamba zakuthengo, m’dziko lonse la Ejipito.

16 Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu.

17 Ndipo tsopano, ndikhululukiretu kulakwa kwanga nthawi ino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andichotsere imfa ino yokha.

18 Ndipo anatuluka kwa Farao, napemba Yehova.

19 Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.

20 Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele amuke.

Chozizwitsa cha 9: Mdima

21 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima padziko la Ejipito, ndiwo mdima wokhudzika.

22 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kuthambo; ndipo munali mdima bii m’dziko lonse la Ejipito masiku atatu;

23 sanaonane, sanaukenso munthu pamalo pake, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israele kudayera m’nyumba zao.

24 Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu aang’ononso.

25 Koma Mose anati, Mutipatsenso m’dzanja mwathu nsembe zophera ndi nsembe zopsereza, kuti timkonzere Yehova Mulungu wathu.

26 Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.

27 Koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo anakana kuwaleka amuke.

28 Ndipo Farao ananena naye, Choka pano, uzichenjera usaonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa.

29 Ndipo Mose anati, Mwanena bwino; sindidzaonanso nkhope yanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/10-fd3a81d3b2320a4b8f2bd04da4aad980.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *