Categories
EKSODO

EKSODO 1

Masautso a ana a Israele mu Ejipito

1 Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa mu Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake:

2 Rubeni, Simeoni, Levi ndi Yuda;

3 Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini;

4 Dani ndi Nafutali, Gadi ndi Asere.

5 Ndipo amoyo onse amene anatuluka m’chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali mu Ejipito.

6 Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi mbadwo uwo wonse.

7 Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.

8 Pamenepo inalowa mfumu yatsopano mu ufumu wa Ejipito, imene siinadziwe Yosefe.

9 Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu.

10 Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m’dzikomo.

11 Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangiraFaraomizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi.

12 Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele.

13 Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa;

14 nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.

Anamwino samvera mfumu

15 Ndipo mfumu ya Aejipito inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifira, dzina la mnzake ndiye Puwa;

16 ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.

17 Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana aamuna akhale ndi moyo.

18 Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana aamunawo akhale ndi moyo?

19 Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.

20 Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu.

21 Ndipo kunatero kuti, popeza anamwino anaopa Mulungu, Iye anawamangitsira mabanja.

22 Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m’mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/1-c487543f057e15449b0be3dbe8f0e5cb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *