Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 8

Akumbuke zokoma zazikulu Mulungu anawachitira

1 Muzisamalira kuchita malamulo onse amene ndikuuzani lero lino, kuti mukhale ndi moyo, ndi kuchuluka, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova analumbirira makolo anu.

2 Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m’chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.

3 Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndimana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.

4 Zovala zanu sizinathe pathupi panu, phazi lanu silinatupe zaka izi makumi anai.

5 Ndipo muzindikire m’mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.

6 Ndipo muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake, ndi kumuopa.

7 Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m’dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe ndi la maiwe akutuluka m’zigwa, ndi m’mapiri;

8 dziko la tirigu ndi barele, ndi mipesa, ndi mikuyu, ndi makangaza; dziko la azitona a mafuta, ndi uchi;

9 dziko loti mudzadyamo mkate wosapereweza; simudzasowamo kanthu; dziko loti miyala yake nja chitsulo, ndi m’mapiri ake mukumbe mkuwa.

10 Ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kuyamika Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko lokomali anakupatsani.

11 Chenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino;

12 kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo;

13 ndipo zitachuluka ng’ombe zanu, ndi nkhosa zanu, atachulukansosilivawanu ndi golide wanu, zitachulukanso zonse muli nazo;

14 mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Ejipito, m’nyumba ya ukapolo;

15 amene anakutsogolerani m’chipululu chachikulu ndi choopsacho, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakutulutsirani madzi m’thanthwe lansangalabwi;

16 amene anakudyetsani m’chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;

17 ndipo munganene m’mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira chuma ichi.

18 Koma mukumbukire Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera chuma; kuti akhazikitsechipanganochake chimene analumbirira makolo anu, monga chikhala lero lino.

19 Ndipo kudzakhala kuti mukaiwalatu Yehova Mulungu wanu, ndi kutsata milungu ina ndi kuitumikira, ndikuchitirani mboni lero lino kuti mudzaonongeka ndithu.

20 Mongaamitunduamene Yehova awaononga pamaso panu, momwemo mudzaonongeka; chifukwa cha kusamvera mau a Yehova Mulungu wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/8-54122929546aa90c150717b099aaf210.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *