Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 7

Awapangira za Akanani ndi zipembedzo zao

1 Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m’dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakatayaamitunduambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;

2 nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwachitira chifundo.

3 Ndipo musakwatitsane nao; musampatse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.

4 Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu ina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.

5 Koma muzichita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.

6 Pakuti inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko.

7 Yehova sanakondwere nanu, ndi kukusankhani chifukwa cha kuchuluka kwanu koposa mitundu ina yonse ya anthu, kapena kuchepera kwanu;

8 koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m’nyumba ya ukapolo, m’dzanja laFaraomfumu ya Aejipito, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.

9 Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusungachipanganondi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.

10 Ndipo awabwezera onse akudana ndi Iye, pamaso pao, kuwaononga; sachedwa naye wakudana ndi Iye, ambwezera pamaso pake.

11 Potero muzisunga malamulo, ndi malemba, ndi maweruzo amene ndikuuzani lero kuwachita.

12 Ndipo kudzakhala, chifukwa cha kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwachita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani chipangano ndi chifundo chimene analumbirira makolo anu;

13 ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukuchulukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi anaankhosa anu, m’dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.

14 Mudzakhala odalitsika koposa mitundu yonse ya anthu; sipadzakhala mwamuna kapena wamkazi wosabala pakati pa inu, kapena pakati pa zoweta zanu.

15 Ndipo Yehova adzakuchotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa zilizonse za Aejipito muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.

16 Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha.

17 Mukadzanena m’mtima mwanu, Amitundu awa andichulukira; ndikhoza bwanji kuwapirikitsa?

18 Musamawaopa; mukumbukire bwino chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Farao, ndi Ejipito wonse;

19 mayesero aakulu maso anu anawapenya, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, zimene Yehova Mulungu wanu anakutulutsani nazo; Yehova Mulungu wanu adzatero nayo mitundu yonse ya anthu imene muwaopa.

20 Komanso Yehova Mulungu wanu adzatumiza mavu pakati pao, kufikira ataonongeka otsalawo, ndi akubisala pamaso panu.

21 Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkulu ndi woopsa.

22 Ndipo Yehova Mulungu wanu adzataya amitundu awa pang’onopang’ono; simuyenera kuwaononga msanga, kuti zingakuchulukireni zilombo.

23 Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka pamaso panu, nadzawapirikitsa ndi kupirikitsa kwakukulu, kufikira ataonongeka.

24 Adzaperekanso mafumu ao m’dzanja mwanu, ndipo muwafafanize maina ao pansi pa thambo; palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga.

25 Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirirasilivandi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.

26 Musamalowa nacho chonyansachi m’nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi nacho; muziipidwa nacho konse, ndi kunyansidwa nacho konse; popeza ndi chinthu choyenera kuonongeka konse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/7-1a62e5a353fb959c52196993a45b2adb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *