Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 34

Imfa ya Mose

1 Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani;

2 ndi Nafutali lonse, ndi dziko la Efuremu, ndi Manase, ndi dziko lonse la Yuda, kufikira nyanja ya m’tsogolo;

3 ndi kumwera, ndi chidikha cha chigwa cha Yeriko, mzinda wa migwalangwa, kufikira ku Zowari.

4 Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m’maso, koma sudzaolokako.

5 Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m’dziko la Mowabu, monga mwa mau a Yehova.

6 Ndipo Iye anamuika m’chigwa m’dziko la Mowabu popenyana ndi Betepeori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwake kufikira lero lino.

7 Ndipo zaka zake za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lake silinachite mdima, ndi mphamvu yake siidaleke.

8 Ndipo ana a Israele analira Mose m’zidikha za Mowabu masiku makumi atatu; potero anatha masiku akulira maliro a Mose.

9 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ake; ndi ana a Israele anamvera iye, nachita monga Yehova adauza Mose.

10 Ndipo sanaukensomnenerimu Israele ngati Mose, amene Yehova anadziwana naye popenyana maso;

11 kunena za zizindikiro ndi zozizwa zonse zimene Yehova anamtumiza kuzichita m’dziko la Ejipito kwaFarao, ndi anyamata ake onse, ndi dziko lake lonse;

12 ndi kunena za dzanja la mphamvu lonse, ndi choopsa chachikulu chonse, chimene Mose anachita pamaso pa Israele wonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/34-e47aa763f7e2ea0c553b6abb35a66127.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *