Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 3

1 Pamenepo tinatembenuka, ndi kubwera kunka njira ya ku Basani; ndipo Ogi mfumu ya Basani anatuluka kukomana nafe, kumenyana nafe nkhondo, iye ndi anthu ake onse, ku Ederei.

2 Ndipo Yehova anati kwa ine, Usamuopa; popeza ndampereka iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake, m’dzanja lako; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene anakhala mu Hesiboni.

3 Potero Yehova Mulungu wathu anaperekanso m’manja mwathu Ogi mfumu ya Basani, ndi anthu ake onse, ndipo tinamkantha kufikira sanamtsalire ndi mmodzi yense.

4 Ndipo muja tinalanda mizinda yake yonse; kunalibe mzinda sitinaulande m’manja mwao, mizinda makumi asanu ndi limodzi, dera lonse la Arigobu, dziko la Ogi mu Basani.

5 Yonseyi ndiyo mizinda yozinga ndi malinga aatali, zitseko, ndi mipiringidzo; pamodzi ndi midzi yambirimbiri yopanda malinga.

6 Ndipo tinaiononga konse, monga umo tinachitira Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi kuononga konse mizinda yonse, amuna, akazi ndi ana.

7 Koma zoweta zonse ndi zofunkha za m’mizinda, tinadzifunkhira tokha.

8 Ndipo muja tinalanda dziko m’manja mwa mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, kuyambira mtsinje wa Arinoni kufikira phiri la Heremoni;

9 (Asidoni alitcha Heremoni Sirioni, koma Aamori alitcha Seniri);

10 mizinda yonse ya kuchidikha, ndi Giliyadi lonse, ndi Basani lonse kufikira ku Saleka ndi Ederei, mizinda ya dziko la Ogi mu Basani.

11 (Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).

12 Ndipo dziko ili tinalilanda muja; kuyambira ku Aroere, wa ku mtsinje wa Arinoni, ndi dera lina la ku mapiri a Giliyadi, ndi mizinda yake, ndinapatsa Arubeni ndi Agadi.

13 Ndi chotsalira cha Giliyadi, ndi Basani lonse, dziko la Ogi, ndinapatsa hafu la fuko la Manase; dziko lonse la Arigobu, pamodzi ndi Basani. (Ndilo lotchedwa dziko la Arefaimu.

14 Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino).

15 Ndipo ndinampatsa Makiri Giliyadi.

16 Koma ndinapatsa Arubeni ndi Agadi kuyambira ku Giliyadi kufikira ku mtsinje wa Arinoni, pakati pa chigwa ndi malire ake, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;

17 ndi chidikha, ndi Yordani ndi malire ake, kuyambira ku Kinereti kufikira ku Nyanja ya Araba, ndiyo Nyanja ya Mchere, patsinde pa Pisiga, kum’mawa.

18 Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele.

19 Koma akazi anu, ndi ana anu, ndi zoweta zanu, (ndidziwa muli nazo zoweta zambiri), zikhale m’mizinda yanu imene ndinakupatsani;

20 kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lija la Yordani; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku cholowa chake, chimene ndinakupatsani.

21 Ndipo ndinauza Yoswa muja, ndi kuti, Maso ako anapenya zonse Yehova Mulungu wanu anawachitira mafumu awa awiri; momwemo Yehova adzachitira maufumu onse kumene muolokerako.

22 Musawaopa popeza Yehova Mulungu wanu, ndiye agwirira inu nkhondo.

23 Ndipo ndinapempha chifundo kwa Yehova nthawi yomwe ija, ndi kuti,

24 Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m’mwamba kapena padziko lapansi wakuchita monga mwa ntchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu?

25 Ndioloketu, ndilione dziko lokomali lili tsidya la Yordani, mapiri okoma aja, ndi Lebanoni.

26 Koma Yehova anakwiya ndi ine, chifukwa cha inu, sanandimvere ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Chikukwanire, usaonjezenso kunena ndi Ine za chinthuchi.

27 Kwera kumwamba ku Pisiga, nukweze maso ako kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, ndi kum’mawa, nuyang’ane ndi maso ako; popeza sudzaoloka Yordani uyo.

28 Koma langiza Yoswa, numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale laolao.

29 Potero tinakhala m’chigwamo pandunji pa Betepeori.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/3-dc539c885085cb44533767f127b19b5d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *