Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 28

Madalitso pa kumvera kwao

1 Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a padziko lapansi;

2 ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.

3 Mudzakhala odala m’mzinda, ndi odala kubwalo.

4 Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.

5 Lidzakhala lodala dengu lanu, ndi choumbiramo mkate wanu.

6 Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala potuluka inu.

7 Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.

8 Yehova adzakulamulirani dalitso m’nkhokwe zanu, ndi m’zonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

9 Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m’njira zake.

10 Ndipo anthu onse a padziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.

11 Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m’zipatso za thupi lanu, ndi m’zipatso za zoweta zanu, ndi m’zipatso za nthaka yanu, m’dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo.

12 Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m’nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.

13 Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita;

14 osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira.

Matemberero pa kusamvera kwao

15 Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.

16 Mudzakhala otembereredwa m’mzinda, ndi otembereredwa pabwalo.

17 Lidzakhala lotembereredwa dengu lanu ndi choumbiramo mkate wanu.

18 Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng’ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.

19 Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa potuluka inu.

20 Yehova adzakutumizirani temberero, chisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukatulutsa dzanja lanu kuchita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika msanga, chifukwa cha zochita inu zoipa, zimene wandisiya nazo.

21 Yehova adzakumamatiritsani mliri, kufikira akakuthani kukuchotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.

22 Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya chifuwa, ndi malungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, chinsikwi ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.

23 Ndipo thambo lanu la pamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndi dziko lili pansi panu ngati chitsulo.

24 Yehova adzasanduliza mvula ya dziko lanu ikhale fumbi ndi phulusa; zidzakutsikirani kuchokera kumwamba, kufikira mwaonongeka.

25 Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.

26 Ndipo mitembo yanu idzakhala chakudya cha mbalame zonse za m’mlengalenga, ndi zilombo zonse za padziko lapansi, ndipo palibe wakuziingitsa.

27 Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo.

28 Yehova adzakukanthani ndi misala, ndi khungu, ndi kuzizwa mumtima;

29 ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.

30 Mudzapalana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m’mwemo; mudzaoka munda wampesa, osalawa zipatso zake.

31 Adzapha ng’ombe yanu, pamaso panu, osadyako inu; adzalanda bulu wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.

32 Adzapereka ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m’maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m’dzanja lanu.

33 Mtundu wa anthu umene simuudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;

34 nimudzakhala oyeruka chifukwa chomwe muchiona ndi maso anu.

35 Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pamutu panu.

36 Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simuudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala.

37 Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi mwambi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.

38 Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang’ono; popeza dzombe lidzazitha.

39 Mudzaoka m’minda yampesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wake, kapena kutchera mphesa zake, popeza mbozi zidzaidya.

40 Mudzakhala nayo mitengo yaazitonam’malire anu onse, osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo ya azitona zidzapululuka.

41 Mudzabala ana aamuna ndi aakazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo.

42 Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zaozao za dzombe.

43 Mlendo wokhala pakati panu adzakulirakulira inu, koma inu mudzacheperachepera.

44 Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mchira.

45 Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake ndi malemba ake amene anakulamulirani;

46 ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati chizindikiro ndi chozizwa, nthawi zonse.

47 Popeza simunatumikire Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima, chifukwa cha kuchuluka zinthu zonse;

48 chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.

49 Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;

50 mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamchitira chifundo mwana;

51 ndipo adzadya zipatso za ng’ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng’ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.

52 Ndipo adzakuzingani m’midzi mwanu monse, kufikira adzagwa malinga anu aatali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m’dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m’midzi mwanu monse, m’dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

53 Ndipo mudzadya chipatso cha thupi lanu, nyama ya ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.

54 Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, diso lake lidzaipira mbale wake, ndi mkazi wa pa mtima wake, ndi ana ake otsalira;

55 osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ake alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m’midzi mwanu monse.

56 Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lake popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lake lidzamuipira mwamuna wa pamtima pake, ndi mwana wake wamwamuna ndi wamkazi;

57 ndicho chifukwa cha matenda akutuluka pakati pa mapazi ake, ndi ana ake adzawabala; popeza adzawadya m’tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m’midzi mwanu.

58 Mukapanda kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi olembedwa m’buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo Yehova Mulungu wanu;

59 Yehova adzachita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwitsa, miliri yaikulu ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa.

60 Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Ejipito, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu.

61 Ndiponso nthenda zonse ndi miliri yonse zosalembedwa m’buku la chilamulo ichi, Yehova adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka.

62 Ndipo mudzatsala anthu pang’ono, mungakhale mudachuluka ngati nyenyezi za m’mwamba; popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu.

63 Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.

64 Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.

65 Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m’maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.

66 Ndipo moyo wanu udzakhala wanjiranjira pamaso panu, ndipo mudzachita mantha usiku ndi usana, osakhazika mtima za moyo wanu.

67 M’mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! Ndi madzulo mudzati, Mwezi utafika m’mawa! Chifukwa cha mantha a m’mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi chifukwa cha zopenya maso anu zimene mudzazipenya.

68 Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Ejipito ndi ngalawa, panjira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogula inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/28-0ef2c8a5fb8f498b65cdcefff9a39fc8.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *