Za kuutsa miyala ya chikumbutso ataoloka Yordani
1 Ndipo Mose ndi akulu a Israele anauza anthu, nati, Sungani malamulo onse ndikuuzani lero.
2 Ndipo kudzali, tsiku lakuoloka inu Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, kuti mudziutsire miyala yaikulu, ndi kuimata ndi njeresa;
3 ndipo mulemberepo mau onse a chilamulo ichi, mutaoloka; kuti mulowe m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, monga Yehova Mulungu wa makolo anu ananena ndi inu.
4 Ndipo kudzali, mutaoloka Yordani, muutse miyala iyi ndikuuzani lero, m’phiri la Ebala, ndi kuimata ndi njeresa.
5 Ndipo komweko mumangire Yehova Mulungu wanu guwa la nsembe, guwa la nsembe lamiyala; musakwezepo pangizo chachitsulo.
6 Mumange guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu lamiyala yosasema; ndi kuperekapo nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu;
7 ndi kuphera nsembe zoyamika, ndi kudyapo, ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
8 Ndipo mulembere pa miyalayi mau onse a chilamulo ichi mopenyeka bwino.
9 Ndipo Mose, ndi ansembe Alevi ananena ndi Israele wonse, ndi kuti, Khalani chete, imvanitu, Israele; lero lino mwasanduka mtundu wa anthu wa Yehova Mulungu wanu.
10 Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita malamulo ake ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino.
Mdalitso ndi temberero ku Gerizimu ndi Ebala
11 Ndipo Mose anauza anthu tsiku lomwelo, ndi kuti,
12 Aimirire awa paphiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordani: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini.
13 Naimirire awa paphiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Asere, ndi Zebuloni, Dani ndi Nafutali.
14 Ndipo ayankhe Alevi ndi kunena kwa amuna onse a Israele, ndi mau omveka.
15 Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m’malo a m’tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti,Amen.
16 Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wake kapena mai wake. Ndi anthu onse anene, Amen.
17 Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wake. Ndi anthu onse anene, Amen.
18 Wotembereredwa wakusokeretsa wakhungu m’njira. Ndi anthu onse anene, Amen.
19 Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.
20 Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wake; popeza wavula atate wake. Ndi anthu onse anene, Amen.
21 Wotembereredwa iye wakugona ndi nyama iliyonse. Ndi anthu onse anene, Amen.
22 Wotembereredwa iye wakugona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa make. Ndi anthu onse anene, Amen.
23 Wotembereredwa iye wakugona ndi mpongozi wake. Ndi anthu onse anene, Amen.
24 Wotembereredwa iye wakukantha mnansi wake m’tseri. Ndi anthu onse anene, Amen.
25 Wotembereredwa iye wakulandira chamwazi chakuti akanthe munthu wosachimwa. Ndi anthu onse anene, Amen.
26 Wotembereredwa iye wosavomereza mau a chilamulo ichi kuwachita. Ndi anthu onse anene, Amen.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/27-b29c8c4ac6a5289845274072baee4c4c.mp3?version_id=1068—