Oletsedwa ku msonkhano wa Yehova
1 Munthu wofulika kapena woduka chiwalo chaumuna, asalowe m’msonkhano wa Yehova.
2 Mwana wa m’chigololo asalowe m’msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wake wakhumi usalowe m’msonkhano wa Yehova.
3 Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m’msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m’msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;
4 popeza sanakumane nanu ndi mkate ndi madzi m’njira muja munatuluka mu Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.
5 Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.
6 Musawafunira mtendere, kapena chowakomera masiku anu onse ku nthawi zonse.
7 Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m’dziko lake.
8 Ana obadwa nao a mbadwo wachitatu alowe m’msonkhano wa Yehova.
9 Nkhondo yanu ikatuluka pa adani anu, mudzisunge kusachita choipa chilichonse.
10 Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera chifukwa chochitika usiku, azituluka kunja kwa chigono, asalowe pakati pa chigono;
11 koma kudzali pofika madzulo, asambe m’madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa chigono.
12 Mukhale nao malo kunja kwa chigono kumene muzimukako kuthengo;
13 nimukhale nacho chokumbira mwa zida zanu; ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe nacho, ndi kutembenuka ndi kufotsera chakutulukacho;
14 popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa chigono chanu kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; chifukwa chake chigono chanu chikhale chopatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.
Za akapolo opulumuka, za achigololo, za okongoletsa mopindulitsa
15 Musamapereka kwa mbuye wake kapolo wopulumuka kwa mbuye wake kuthawira kwa inu;
16 akhale nanu, pakati panu, ku malo asankhako iye m’mudzi mwanu mwina momkonda; musamamsautsa.
17 Pasakhale mkazi wachigololo pakati pa ana aakazi a Israele, kapena wachigololo pakati pa ana aamuna a Israele.
18 Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu kulowa nazo m’nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha chowinda chilichonse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.
19 Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndalama, phindu la chakudya, phindu la kanthu kalikonse kokongoletsa.
20 Mukongoletse mlendo mopindulitsa; koma mbale wanu musamamkongoletsa mopindulitsa, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni mwa zonse muzigwira ndi dzanja lanu, m’dziko limene mulowamo kulilandira.
21 Mukawindira Yehova Mulungu wanu chowinda, musamachedwa kuchichita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ichi ndithu ndipo mukadachimwako.
22 Koma mukapanda kulonjeza chowinda, mulibe kuchimwa.
23 Chotuluka pa milomo yanu muchisamalire ndi kuchichita; monga munalonjezera Yehova Mulungu wanu, chopereka chaufulu munachilonjeza pakamwa panu.
24 Mukalowa m’munda wampesa wa mnansi wanu, mudyeko mphesa ndi kukhuta nazo monga mufuna eni; koma musaika kanthu m’chotengera chanu.
25 Mukalowa m’tirigu wosasenga wa mnansi wanu, mubudule ngala ndi dzanja lanu, koma musasengako ndi chisenga tirigu wachilili wa mnansi wanu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/23-fce006c3bc394350bd23b083770edc37.mp3?version_id=1068—