1 Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kunka kuchipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri.
2 Ndipo Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,
3 Yakwanira nthawi yakupaza inu phiri ili; tembenukani kunka kumpoto.
4 Ndipo uuze anthu, ndi kuti, Mukapite kubzola malire a abale anu, ana a Esau okhala mu Seiri; ndipo adzakuopani; muchenjere ndithu;
5 musalimbana nao; popeza sindikupatsakoni dziko lao, pangakhale popondapo phazi lanu ai; pakuti ndapatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake.
6 Mugulane nao chakudya ndi ndalama, kuti mudye; mugulane naonso madzi kuti mumwe.
7 Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m’chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowe kanthu.
8 Potero tinapitirira abale athu, ana a Esau okhala mu Seiri, njira ya chidikha, ku Elati ndi ku Eziyoni-Gebere. Pamenepo tinatembenuka ndi kudzera njira ya chipululu cha Mowabu.
9 Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao.
10 (Aemimu anakhalamo kale, ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, ngati Aanaki.
11 Anawayesa iwonso Arefaimu, monga Aanaki; koma Amowabu awatcha Aemimu.
12 Ndipo Ahori anakhala mu Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m’malo mwao; monga Israele anachitira dziko lakelake, limene Yehova anampatsa).
13 Ukani tsopano, olokani mtsinje wa Zeredi. Ndipo tinaoloka mtsinje wa Zeredi.
14 Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m’chigono, monga Yehova adawalumbirira.
15 Komanso dzanja la Yehova linatsutsana nao, kuwaononga m’chigono, kufikira adawatha.
16 Ndipo kunali, atatha kufa amuna onse ankhondo mwa anthu,
17 Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,
18 Lero lomwe utumphe malire a Mowabu, ndiwo Ari.
19 Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawavuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lakolako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale laolao.
20 (Ilinso aliyesa dziko la Arefaimu; Arefaimu anakhalamo kale; koma Aamoni awatcha Azamzumimu;
21 ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m’malo mwao;
22 monga Iye anachitira ana a Esau, akukhala mu Seiri, pamene anaononga Ahori pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m’malo mwao kufikira lero lomwe.
23 Kunena za Aavimu akukhala m’midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m’malo mwao).
24 Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, Mwamori, ndi dziko lake m’dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.
25 Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.
26 Ndipo ndinatuma amithenga ochokera ku chipululu cha Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti,
27 Ndipitire m’dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere,
28 Undigulitse chakudya ndi ndalama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndalama, kuti ndimwe; chokhachi ndipitire choyenda pansi;
29 monga anandichitira ana a Esau akukhala mu Seiri, ndi Amowabu akukhala mu Ari; kufikira nditaoloka Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa.
30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m’dzanja lanu, monga lero lino.
31 Ndipo Yehova anati kwa ine, Taona, ndayamba kupereka Sihoni ndi dziko lake pamaso pako; yamba kulandira dziko lake likhale lakolako.
32 Pamenepo Sihoni anatuluka kukomana nafe, iye ndi anthu ake onse, kumenyana nafe nkhondo ku Yahazi.
33 Ndipo Yehova Mulungu wathu anampereka iye pamaso pathu; ndipo tinamkantha, iye ndi ana ake aamuna ndi anthu ake onse.
34 Ndipo muja tinalanda mizinda yake yonse; ndipo tinaononga konse mizinda yonse, amuna ndi akazi ndi ana; sitinasiyapo ndi mmodzi yense.
35 Zoweta zokha tinadzifunkhira, pamodzi ndi zofunkha za mizinda tidailanda.
36 Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mzinda wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.
37 Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikize; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi mizinda ya kumapiri, ndi kwina kulikonse Yehova Mulungu wathu anatiletsa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/2-6f4dc7a4f274178cf7e741faa217c2f5.mp3?version_id=1068—