Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 1

Mose awafotokozera za ulendo wao m’chipululu

1 Awa ndi mau amene Mose ananena kwa Israele wonse, tsidya la Yordani m’chipululu, m’chidikha cha pandunji pa Sufu, pakati pa Parani, ndi Tofele, ndi Labani, ndi Hazeroti, ndi Dizahabu.

2 Ulendo wake wochokera ku Horebu wofikira ku Kadesi-Baranea, wodzera njira ya phiri la Seiri, ndiwo wa masiku khumi ndi limodzi.

3 Ndipo kunali, chaka cha makumi anai, mwezi wakhumi ndi umodzi, tsiku loyamba la mweziwo, Mose ananena ndi ana a Israele, monga mwa zonse Yehova adamlamulira awauze;

4 atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, wakukhala mu Asitaroti, ku Ederei.

5 Tsidya lija la Yordani, m’dziko la Mowabu, Mose anayamba kufotokozera chilamulo ichi, ndi kuti,

6 Yehova Mulungu wathu ananena ndi ife mu Horebu, ndi kuti Yakwanira nthawi yokhala inu m’phiri muno;

7 bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kuchidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwera, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebanoni, kufikira mtsinje waukulu wa Yufurate.

8 Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.

9 Ndipo muja ndinanena ndi inu, ndi kuti, Sinditha ine kukunyamulani ndekha;

10 Yehova Mulungu wanu anakuchulukitsani, ndipo taonani, lero muchuluka ngati nyenyezi za kumwamba.

11 Yehova Mulungu wa makolo anu, achulukitsire chiwerengero chanu chalero ndi chikwi chimodzi, nakudalitseni monga Iye ananena nanu!

12 Ndikasenza bwanji ndekha kupsinya kwanu, ndi katundu wanu, ndi kulimbana kwanu?

13 Dzifunireni amuna anzeru, ndi ozindikira bwino, ndi odziwika mwa mafuko anu, ndipo ndidzawaika akhale akulu anu.

14 Pamenepo munandiyankha ndi kuti, Mau mwanenawa ndi abwino kuwachita.

15 Potero ndinatenga akulu a mafuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akulu anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi asanu, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mafuko anu.

16 Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wake, ndi mlendo wokhala naye.

17 Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang’ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.

18 Ndipo ndinakuuzani muja zonse muyenera kuzichita.

19 Pamenepo tinayenda ulendo kuchokera ku Horebu, ndi kubzola m’chipululu chachikulu ndi choopsa chija chonse munachionachi, panjira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi-Baranea.

20 Ndipo ndinati kwa inu, Mwafikira mapiri a Aamori, amene Yehova Mulungu wathu atipatsa.

21 Taonani, Yehova Mulungu wanu wapatsa dzikoli pamaso panu; kwerakoni, landirani, monga Yehova Mulungu wa makolo anu, wanena ndi inu; musamachita mantha, musamatenga nkhawa.

22 Ndipo munayandikiza kwa ine inu nonse, ndi kuti, Titumize amuna atitsogolere, kuti akatizondere dziko ndi kutibwezera mau akunena za njira ya kukwera nayo ife pomka komwemo, ndi za mizinda yoti tidzafikako.

23 Ndipo chinandikomera chinthu ichi; ndipo ndinatenga amuna khumi ndi awiri a inu, fuko limodzi mwamuna mmodzi;

24 amenewa anatembenuka nakwera kumapiri nalowa ku chigwa cha Esikolo, nachizonda.

25 Ndipo anatengako zipatso za dzikoli m’manja mwao, natsikira nazo kwa ife, natibwezera mau ndi kuti, Dzikoli Yehova Mulungu wathu atipatsa ndi labwino.

26 Koma simunafune kukwerako, ndipo munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu.

27 Ndipo munadandaula m’mahema mwanu, ndi kuti, Popeza anatida Yehova, Iye anatitulutsa m’dziko la Ejipito, kutipereka m’manja mwa Aamori, ationonge.

28 Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo aakulu ndi aatali akuposa ife; mizinda ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m’mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.

29 Pamenepo ndinati kwa inu, Musamaopsedwa, musamachita mantha nao.

30 Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, Iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu;

31 ndi kuchipululu, kumene munapenya kuti Yehova Mulungu wanu anakunyamulani, monga anyamula mwana wake wamwamuna, m’njira monse munayendamo, kufikira mutalowa m’malo muno.

32 Koma m’chinthu ichi simunakhulupirire Yehova Mulungu wanu,

33 amene anakutsogolerani m’njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi moto usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.

34 Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, nakwiya, nalumbira, ndi kuti,

35 Palibe mmodzi wa anthu awa a mbadwo uno woipa adzaona dziko lokomalo ndinalumbira kupatsa makolo anuli.

36 Koma Kalebe mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ake; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.

37 Yehova anakwiya ndi inenso chifukwa cha inu, ndi kuti, Iwenso sudzalowamo.

38 Yoswa mwana wa Nuni, wakuima pamaso pako, iye adzalowamo; umlimbitse mtima; popeza iye adzalandiritsa Israele.

39 Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa chabwino kapena choipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.

40 Koma inu, bwererani, mukani ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

41 Pamenepo munayankha ndi kunena ndi ine, Tachimwira Yehova, tidzakwera ndi kuthira nkhondo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu atiuza. Ndipo munadzimangira munthu yense zida zake za nkhondo, nimunakonzeka kukwera kunka kumapiri.

42 Koma Yehova anati kwa ine, Nena nao, Musakwerako, kapena kuthira nkhondo; popeza sindili pakati panu; angakukantheni adani anu.

43 Pamene ndinanena ndi inu simunamvere; koma munatsutsana nao mau a Yehova ndi kuchita modzikuza, nimunakwera kunka kumapiri.

44 Ndipo Aamori, akukhala m’mapiri muja, anatuluka kukomana ndi inu, nakupirikitsani, monga zimachita njuchi, nakukanthani mu Seiri, kufikira ku Horoma.

45 Ndipo munabwerera ndi kulira pamaso pa Yehova; koma Yehova sanamvere mau anu, kapena kukutcherani khutu.

46 Potero munakhala mu Kadesi masiku ambiri, monga mwa masiku munakhalako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/1-cc1ccbb8fbb00bf5a88eed87ee5245ec.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *