Categories
DANIELE

DANIELE 12

Nthawi ya chimaliziro, mau otsekedwa

1 Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhale yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m’buku.

2 Ndipo ambiri a iwo ogona m’fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha.

3 Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.

4 Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.

5 Pamenepo ine Daniele ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo awiri ena, wina m’mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzake m’mphepete mwa mtsinje tsidya lija.

6 Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti?

7 Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.

8 Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani?

9 Ndipo anati, Pita Daniele; pakuti mauwo atsekedwa, nakhomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro.

10 Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.

11 Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, ndipo chidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

12 Wodala iye amene ayembekeza, nafikira kumasiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.

13 Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m’gawo lako masiku otsiriza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/12-843acd5848983070b6ca8d2f6993b101.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *