Categories
DANIELE

DANIELE 10

Daniele aona masomphenya oopsa, mngelo amlimbikitsa

1 Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo.

2 Masiku aja ine Daniele ndinali kulira masabata atatu amphumphu.

3 Chakudya chofunika osachidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu.

4 Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi woyamba, pokhala ine m’mphepete mwa mtsinje waukulu, ndiwo Tigrisi,

5 ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wovala bafuta, womanga m’chuuno ndi golide woona wa ku Ufazi;

6 thupi lake lomwe linanga berulo, ndi nkhope yake ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ake ngati nyali zamoto, ndi manja ake ndi mapazi ake akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ake kunanga phokoso la aunyinji.

7 Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala.

8 Momwemo ndinatsala ndekha, ndipo ndinaona masomphenya aakuluwa, koma wosakhala ndi mphamvu ine; pakuti kukoma kwanga kunasandulika chivundi mwa ine, wosakhalanso ndi chimphamvu ine.

9 Ndipo ndinamva kunena kwa mau ake, ndipo pamene ndinamva kunena kwa mau ake ndinagwidwa ndi tulo tatikulu pankhope panga, nkhope yanga pansi.

10 Ndipo taonani, linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga.

11 Nati kwa ine, Daniele, munthu wokondedwatu iwe, tazindikira mau ndilikunena ndi iwe, nukhale chilili; pakuti ndatumidwa kwa iwe tsopano. Ndipo pamene adanena mau awa kwa ine ndinaimirira ndi kunjenjemera.

12 Pamenepo anati kwa ine, Usaope Daniele; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako.

13 Koma kalonga wa ufumu wa Persiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaele, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Persiya.

14 Ndadzera tsono kukuzindikiritsa chodzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m’tsogolo.

15 Ndipo atanena ndi ine monga mwa mau awa, ndinaweramitsa nkhope yanga pansi ndi kukhala duu.

16 Ndipo taonani, wina wakunga ana a anthu anakhudza milomo yanga; pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndi kunena naye woima popenyana nane, Mbuye wanga, chifukwa cha masomphenyawo zowawa zanga zandibwerera, ndipo ndilibenso mphamvu.

17 Pakuti mnyamata wa mbuye wanga inu akhoza bwanji kulankhula ndi mbuye wanga inu? Pakuti ine tsopano apa mulibenso mphamvu mwa ine, osanditsaliranso mpweya.

Nkhondo ya pakati pa Persiya ndi Grisi

18 Pamenepo anandikhudzanso wina, maonekedwe ake ngati munthu, nandilimbikitsa ine.

19 Nati, Munthu wokondedwatu iwe, Usaope, mtendere ukhale nawe; limbika, etu limbika. Ndipo pamene ananena ndi ine ndinalimbikitsidwa, ndinati, Anene mbuye wanga; pakuti mwandilimbikitsa.

20 Pamenepo anati, Kodi udziwa chifukwa choti ndakudzera? Ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Persiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Agriki.

21 Koma ndidzakufotokozera cholembedwa pa lemba la choonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaele kalonga wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DAN/10-34ad840c4677fa3e7f4ab846b2212453.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *