Mau Oyamba
Buku la
Chivumbulutso
lidalembedwa pa nthawi ina pamene Akhristu ankazunzidwa chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu kuti Iye ndi Ambuye. Wolemba bukuli akufuna kuwalimbitsa mtima Akhristu onse kuti akhale okhulupirika kwa Ambuye pamene akukumana ndi mavuto komanso mazunzo.
Pafupi mau onse a m’bukuli akamba za zobisika ndi zinsinsi zina ndi zina zimene mlembiyo adazimva ndi kuziwona m’masomphenya; ndipo amazilongosola mwa njira ya mafanizo ndi mau ophiphiritsa, kotero kuti Akhristu okha pa masiku akalewo ankamvetsapo mauwo, chonsecho anzao onse akunja sankatha kutulukira tanthauzo lake lenileni. Mfundo zake za bukuli amazikamba mobwerezabwereza mwa njira zosiyanasiyana, potsata zomwe zija anaziwona m’masomphenya; motero nkwapatali kutanthauzira imodziimodzi mwa nkhani zonsezo movemerezana. Komabe phunziro lalikulu lopezeka m’bukuli nlakuti, lidzafika tsiku lina pamene, kudzera mwa Khristu Ambuye, Mulungu adzagonjetsa kotheratu adani ake onse ndi Satana yemwe; ndipo adzapereka mphotho kwa anthu ake okhulupirika, adzawadalitsa poti adzakonzanso zonse kuti zikhale zatsopano.
Za mkatimu
Yohane apereka moni kwa mipingo isanu ndi iwiri 1.1-8
Aona Khristu m’masomphenya 1.9-20
Makalata olembera mipingo isanu ndi iwiri 2.1—3.22
Za m’mene amapembedzera Kumwamba 4.1-11
Za Mwanawankhosa ndi buku lomatidwa ndi zimatiro 5.1—8.1
Za angelo asanu ndi awiri oliza malipenga 8.2—11.19
Za chinjoka ndi zilombo ziwiri 12.1—13.18
Zina ndi zina zooneka m’masomphenya 14.1—15.8
Za mbale zisanu ndi ziwiri za ukali wa Mulungu 16.1-21
Za kugwa kwa Babiloni ndi kugonjetsedwa kwa Satana 17.1—20.10
Za chiweruzo chotsiriza 20.11-15
Za dziko latsopano ndi Yerusalemu watsopano 21.1—22.5
Mau otsiriza: za kubwera kwa Yesu 22.6-21