Buku losindikizika ndi zosindikiza zisanu ndi ziwiri. Mwanawankhosa yekha ayenera kulitsegula
1 Ndipo ndinaona m’dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m’kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.
2 Ndipo ndinaonamngelowamphamvu wakulalikira ndi mau aakulu, Ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikiro zake?
3 Ndipo sanathe mmodzi mu Mwamba, kapena padziko, kapena pansi padziko kutsegula pabukupo, kapena kulipenya.
4 Ndipo ndinalira kwambiri, chifukwa sanapezeke mmodzi woyenera kutsegula bukulo, kapena kulipenya;
5 ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m’fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.
6 Ndipo ndinaona pakati pa mpando wachifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akulu,Mwanawankhosaali chilili ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m’dziko lonse.
7 Ndipo anadza, nalitenga kudzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu.
8 Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.
9 Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,
10 ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.
11 Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva mau a angelo ambiri pozinga mpando wachifumu, ndi zamoyo ndi akulu; ndipo mawerengedwe ao anali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi;
12 akunena ndi mau aakulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko.
13 Ndipo cholengedwa chilichonse chili m’mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m’nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi.
14 Ndipo zamoyo zinai zinati,Amen. Ndipo akuluwo anagwa pansi nalambira.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/5-1a3c586f1556b4a4292da3a3a3a6094d.mp3?version_id=1068—