Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 4

Masomphenya a mpando wachifumu wa Mulungu, akulu makumi awiri ndi anai, ndi zamoyo zinai

1 Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka mu Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga lakulankhula ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m’tsogolomo.

2 Pomwepo ndinakhala mwa Mzimu; ndipo, taonani padaikika mpando wachifumu mu Mwamba ndi pa mpandowo padakhala wina;

3 ndipo maonekedwe a Iye wokhalapo anafanana ndi mwala wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati smaragido.

4 Ndipo pozinga mpando wachifumu mipando yachifumu makumi awiri mphambu inai, ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi awiri mphambu anai, atavala zovala zoyera, ndi pamitu pao akorona agolide.

5 Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;

6 ndipo kumpandowo, ngati nyanja yagalasi yonga krustalo; ndipo pakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzala ndi maso kutsogolo ndi kumbuyo.

7 Ndipo chamoyo choyamba chinafanana nao mkango, ndi chamoyo chachiwiri chinafanana ndi mwanawang’ombe, ndi chamoyo chachitatu chinali nayo nkhope yake ngati ya munthu, ndi chamoyo chachinai chidafanana ndi chiombankhanga chakuuluka.

8 Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m’katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.

9 Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi uyamiko kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, kwa Iye wakukhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi,

10 akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena,

11 Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/4-84d53023eff90426f63f347aba9f3a83.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *