Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 2

Kalata ya kwa Mpingo wa ku Efeso

1 KwamngelowaMpingowa ku Efeso lemba:

Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m’dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide:

2 Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sungathe kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okhaatumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;

3 ndipo uli nacho chipiriro, ndipo walola chifukwa cha dzina langa, wosalema.

4 Koma ndili nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya chikondi chako choyamba.

5 Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.

6 Koma ichi uli nacho, kuti udana nazo ntchito zaAnikolai, zimene Inenso ndidana nazo.

7 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.

Kalata yachiwiri, ya kwa Mpingo wa ku Smirina

8 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smirina lemba:

Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo:

9 Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatusunagogewaSatana.

10 Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.

11 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene apambana sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.

Kalata yachitatu, ya kwa Mpingo wa ku Pergamo

12 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba:

Izi anena Iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konsekonse:

13 Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m’masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.

14 Komatu ndili nazo zinthu pang’ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.

15 Kotero uli nao akugwira chiphunzitso cha Anikolai momwemonso.

16 Chifukwa chake lapa; ukapanda kutero ndidza kwa iwe posachedwa, ndipo ndidzachita nao nkhondo ndi lupanga la m’kamwa mwanga.

17 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsamanaobisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.

Kalata yachinai, ya kwa Mpingo wa ku Tiatira

18 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba:

Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:

19 Ndidziwa ntchito zako, ndi chikondi, ndi chikhulupiriro, ndi utumiki, ndi chipiriro chako, ndi kuti ntchito zako zotsiriza zichuluka koposa zoyambazo.

20 Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekhamneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.

21 Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chigololo chake.

22 Taona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akuchita chigololo naye kuwalonga m’chisautso chachikulu, ngati salapa iwo ndi kuleka ntchito zake.

23 Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.

24 Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiatira, onse amene alibe chiphunzitso ichi, amene sanazindikire zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina.

25 Koma chimene muli nacho, gwirani kufikira ndikadza.

26 Ndipo iye amene apambana, ndi iye amene asunga ntchito zanga kufikira chitsiriziro, kwa iye ndidzapatsa ulamuliro wa paamitundu;

27 ndipo adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale; monga Inenso ndalandira kwa Atate wanga;

28 ndipo ndidzampatsa iye nthanda.

29 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/2-c768222bb09d3ef2112c268cabf4c83d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *