Kupasula kwa Babiloni. Chimwemwe ndi mayamiko mu Mwamba
1 Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena,Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;
2 pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.
3 Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wake ukwera kunthawi za nthawi.
4 Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kunena,Amen; Aleluya.
5 Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, aang’ono ndi aakulu.
6 Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.
7 Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati waMwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.
8 Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbuu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.
9 Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa kuphwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.
10 Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.
Khristu agonjetsa chilombo ndi mneneri wonyenga
11 Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.
12 Ndipo maso ake ali lawi la moto, ndi pamutu pake pali nduwira zachifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha.
13 Ndipo avala chovala chowazidwa mwazi; ndipo atchedwa dzina lake, Mau a Mulungu.
14 Ndipo magulu a nkhondo okhala mu Mwamba anamtsata Iye, okwera pa akavalo oyera, ovala bafuta woyera woti mbuu.
15 Ndipo m’kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.
16 Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.
17 Ndipo ndinaonamngeloalikuima m’dzuwa; ndipo anafuula ndi mau aakulu akunena ndi mbalame zonse zakuuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani kuphwando la Mulungu wamkulu,
18 kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi aang’ono ndi aakulu.
19 Ndipo ndinaona chilombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo ao, osonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake.
20 Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m’nyanja yamoto yakutentha ndisulufure:
21 ndipo otsalawa anaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo, ndilo lotuluka m’kamwa mwake; ndipo mbalame zonse zinakhuta ndi nyama zao.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/19-c254fa4c315d4a9d42a4f1ec2b47773e.mp3?version_id=1068—