Za mkazi ndi chinjoka
1 Ndipo chizindikiro chachikulu chinaoneka m’mwamba; mkazi wovekedwa dzuwa, ndi mwezi kumapazi ake, ndi pamutu pake korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri;
2 ndipo anali ndi pakati; ndipo afuula alimkubala, ndi kumva zowawa zakubala.
3 Ndipo chinaoneka chizindikiro china m’mwamba taonani, chinjoka chofiira, chachikulu, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pake nduwira zachifumu zisanu ndi ziwiri.
4 Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam’mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala icho chikalikwire mwana wake.
5 Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi kumpando wachifumu wake.
6 Ndipo mkazi anathawira kuchipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.
7 Ndipo munali nkhondo m’mwamba. Mikaele ndiangeloake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo;
8 ndipo sichinapambane, ndipo sanapezekenso malo ao m’mwamba.
9 Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndiSatana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.
10 Ndipo ndinamva mau aakulu mu Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro waKhristuwake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.
11 Ndipo iwo anampambana iye chifukwa cha mwazi waMwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonde moyo wao kungakhale kufikira imfa.
12 Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.
13 Ndipo pamene chinjoka chinaona kuti chinaponyedwa pansi kudziko, chinazunza mkazi amene adabala mwana wamwamuna.
14 Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a chiombankhanga chachikulu, kuti akaulukire kuchipululu, ku mbuto yake, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.
15 Ndipo njokayo inalavula m’kamwa mwake, madzi ngati mtsinje, potsata mkazi, kuti mkaziyo akakokoleredwe nao.
16 Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m’kamwa mwake, nilinameza madzi a mtsinje amene chinjoka chinalavula m’kamwa mwake.
17 Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, ndipo chinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.
18 Ndipo chinjokacho chinakaimirira m’mbali mwa nyanja.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/12-7a0adf1a96d270b2883b6434d6bd04c4.mp3?version_id=1068—