Categories
CHIVUMBULUTSO

CHIVUMBULUTSO 1

Choneneratu bukuli

1 Chivumbulutso cha YesuKhristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwamngelowake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;

2 amene anachita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, zonse zimene adaziona.

3 Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.

Mau a kwa Mipingo isanu ndi iwiri ya mu Asiya

4 Yohane kwaMipingoisanu ndi iwiri mu Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake;

5 ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;

6 natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi.Amen.

7 Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu.Amen.

8 Ine ndineAlefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.

Yohane pa chisumbu cha Patimosi. Amlembetsa masomphenya

9 Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m’chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu.

10 Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,

11 ndi kuti, Chimene upenya, lemba m’buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.

12 Ndipo ndinacheuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndinaona zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide;

13 ndipo pakati pa zoikaponyalizo wina wongaMwana wa Munthuatavala chofikira kumapazi ake, atamangira lamba lagolide pachifuwa.

14 Ndipo tsitsi la pamutu pake linali loyera ngati ubweya woyera, ngati chipale chofewa; ndi maso ake ngati lawi la moto;

15 ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m’ng’anjo; ndi mau ake ngati mkokomo wa madzi ambiri.

16 Ndipo m’dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m’kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.

17 Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,

18 ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.

19 Chifukwa chake lemba zimene unaziona, ndi zimene zilipo, ndi zimene zidzaoneka m’tsogolomo;

20 chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/1-4e3de28f8fa0a8669be5a0559b81fe80.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *