Categories
AROMA

AROMA 9

Paulo alirira kusamvera kwa Israele

1 Ndinena zoona mwaKhristu, sindinama ai, chikumbumtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,

2 kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.

3 Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;

4 ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira mu Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;

5 a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse.Amen.

Ulamuliro wa Mulungu wakusankha ena

6 Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;

7 kapena chifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isaki, mbeu yako idzaitanidwa.

8 Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yake.

9 Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana.

10 Ndipo si chotero chokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isaki;

11 pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo,

12 chotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono.

13 Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.

14 Ndipo tsono tidzatani? Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ai.

15 Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni.

16 Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo.

17 Pakuti lembo linena kwaFarao, Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe padziko lonse lapansi.

18 Chotero Iye achitira chifundo amene Iye afuna, ndipo amene Iye afuna amuumitsa mtima.

19 Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza chifuniro chake?

20 Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero?

21 Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi?

22 Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko?

23 Ndi kuti Iye akadziwitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene Iye anazikonzeratu kuulemerero,

24 ndi ife amenenso Iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthuamitundu?

25 Monga atinso mwa Hoseya,

Amene sanakhale anthu anga, ndidzawatcha anthu anga;

ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.

26 Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo,

Simuli anthu anga ai,

pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo.

27 Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti,

Ungakhale unyinji wa ana a Israele

ukhala monga mchenga wa kunyanja,

chotsalira ndicho chidzapulumuka.

28 Pakuti Ambuye adzachita mau ake padziko lapansi, kuwatsiriza mwachidule.

29 Ndipo monga Yesaya anati kale,

Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyire ife mbeu,

tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora.

30 Chifukwa chake tidzatani? Kuti amitundu amene sanatsate chilungamo, anafikira chilungamo, ndicho chilungamo cha chikhulupiriro;

31 koma Israele, potsata lamulo la chilungamo, sanafikile lamulolo.

32 Chifukwa chanji? Chifukwa kuti sanachitsate ndi chikhulupiriro, koma monga ngati ndi ntchito. Anakhumudwa pamwala wokhumudwitsa;

33 monganso kwalembedwa, kuti,

Onani, ndikhazika muZiyonimwala wakukhumudwa nao,

ndi thanthwe lophunthwitsa;

ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/9-2655e52f3220d2f89befdc76f3743a7c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *