Okhulupirira akwatiwa ndi Khristu
1 Nanga kodi simudziwa, abale, pakuti ndilankhula ndi anthu akudziwa lamulo, kuti lamulolo lichita ufumu pa munthu nthawi zonse iye ali wamoyo?
2 Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.
3 Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
4 Chotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi laKhristu; kuti mukakhale ake a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso.
5 Pakuti pamene tinali m’thupi, zilakolako za machimo, zimene zinali mwa chilamulo, zinalikuchita m’ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso.
6 Koma tsopano tinamasulidwa kuchilamulo, popeza tinafa kwa ichi chimene tinagwidwa nacho kale; chotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m’chilembo chakale ai.
Malamulo aonetsa zoipa
7 Pamenepo tidzatani? Kodi chilamulo chili uchimo? Msatero ai. Koma ine sindikadazindikira uchimo, koma mwa lamulo ndimo; pakuti sindikadazindikira chilakolako sichikadati chilamulo, Usasirire;
8 koma uchimo, pamene unapeza chifukwa, unachita m’kati mwanga zilakolako zonse mwa lamulo; pakuti popanda lamulo uchimo uli wakufa.
9 Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.
10 Ndipo lamulo, limene linali lakupatsa moyo, ndinalipeza lakupatsa imfa.
11 Pakuti uchimo, pamene unapeza chifukwa mwa lamulo, unandinyenga ine, ndi kundipha nalo.
12 Chotero chilamulo chili choyera, ndi chilangizo chake nchoyera, ndi cholungama, ndi chabwino.
Kulimbana m’kati mwanga
13 Ndipo tsopano chabwino chija chinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma uchimo, kuti uoneke kuti uli uchimo, wandichitira imfa mwa chabwino chija; kuti uchimo ukakhale wochimwitsa ndithu mwa lamulo.
14 Pakuti tidziwa kuti chilamulo chili chauzimu; koma ine ndili wathupi, wogulitsidwa kapolo wa uchimo.
15 Pakuti chimene ndichita sindichidziwa; pakuti sindichita chimene ndifuna, koma chimene ndidana nacho, ndichita ichi.
16 Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, ndivomerezana nacho chilamulo kuti chili chabwino.
17 Ndipo tsopano si ine ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m’kati mwanga ndiwo.
18 Pakuti ndidziwa kuti m’kati mwanga, ndiko m’thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza.
19 Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.
20 Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, si ndinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m’kati mwanga ndiwo.
21 Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko.
22 Pakuti monga mwa munthu wa m’kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu:
23 koma ndiona lamulo lina m’ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la uchimo m’ziwalo zanga.
24 Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?
25 Ndiyamika Mulungu, mwa YesuKhristuAmbuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/7-7bcd7c3c6c367435646a8a25a1011f7a.mp3?version_id=1068—