Categories
AROMA

AROMA 6

Khristu anatithyolera mphamvu ya zoipa

1 Chifukwa chake tidzatani? Tidzakhalabe mu uchimo kodi, kuti chisomo chichuluke?

2 Msatero ai. Ife amene tili akufa ku uchimo, tidzakhala bwanji chikhalire m’menemo?

3 Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwaKhristuYesu; tinabatizidwa mu imfa yake?

4 Chifukwa chake tinaikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m’moyo watsopano.

5 Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’chifanizidwe cha imfa yake, koteronso tidzakhala m’chifanizidwe cha kuuka kwake;

6 podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo;

7 pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuuchimo.

8 Koma ngati ife tinafa ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi Iye;

9 podziwa kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siichitanso ufumu pa Iye.

10 Pakuti pakufa Iye, atafa ku uchimo kamodzi; ndipo pakukhala Iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu.

11 Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.

12 Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m’thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake:

13 ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.

14 Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a chisomo.

Ife ndife akapolo a Mulungu

15 Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitili a lamulo, koma a chisomo? Msatero ai.

16 Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?

17 Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho;

18 ndipo pamene munamasulidwa kuuchimo, munakhala akapolo a chilungamo.

19 Ndilankhula manenedwe a anthu, chifukwa cha kufooka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a chonyansa ndi a kusaweruzika kuti zichite kusaweruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a chilungamo kuti zichite chiyeretso.

20 Pakuti pamene inu munali akapolo a uchimo, munali osatumikira chilungamo.

21 Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m’zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chili imfa.

22 Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.

23 Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/6-0f1725adfc408b320f4274140008d737.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *