Categories
AROMA

AROMA 5

Zipatso za chikhulupiriro

1 Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu YesuKhristu;

2 amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m’chisomo ichi m’mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m’chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.

3 Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m’zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;

4 ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

5 ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m’mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

6 Pakuti pamene tinali chikhalire ofooka, pa nyengo yake Khristu anawafera osapembedza.

7 Pakuti ndi chivuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino.

8 Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.

9 Ndipo tsono popeza tinayesedwa olungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo.

10 Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.

11 Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso.

Uchimo unalowa ndi Adamu, chilungamo ndi Khristu

12 Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.

13 Pakuti kufikira nthawi ya lamulo uchimo unali m’dziko lapansi; koma uchimo suwerengedwa popanda lamulo.

14 Komatu imfa inachita ufumu kuyambira kwaAdamukufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sanachimwe monga machimwidwe ake a Adamu, ndiye fanizo la wakudzayo.

15 Koma mphatso yaulere siilingana ndi kulakwa. Pakuti ngati ambiriwo anafa chifukwa cha kulakwa kwa mmodziyo, makamaka ndithu chisomo cha Mulungu, ndi mphatso yaulere zakuchokera ndi munthu mmodziyo Yesu Khristu, zinachulukira anthu ambiri.

16 Ndipo mphatso siinadze monga mwa mmodzi wakuchimwa, pakuti mlandu ndithu unachokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere ichokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama.

17 Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inachita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kuchuluka kwake kwa chisomo ndi kwa mphatso ya chilungamo, adzachita ufumu m’moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Khristu.

18 Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse.

19 Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama.

20 Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa;

21 kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/5-96bd378298c85b9755d569d11db7ec9d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *