Categories
AROMA

AROMA 15

Khristu chitsanzo cha kusamalirana kumene

1 Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.

2 Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.

3 Pakuti Khristunso sanadzikondweretse yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa Ine.

4 Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.

5 Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwaKhristuYesu;

6 kuti nonse pamodzi, m’kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

7 Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.

8 Ndipo ndinena kuti Khristu anakhala mtumiki wamdulidwe, chifukwa cha choonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,

9 ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa,

Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani Inu

pakati pa anthuamitundu,

ndidzaimbira dzina lanu.

10 Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake.

11 Ndiponso,

Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse;

ndipo anthu onse amtamande.

12 Ndiponso, Yesaya ati,

Padzali muzu wa Yese,

ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu;

Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.

13 Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m’kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Utumwi wake ndi zotsimikiza mtima za Paulo

14 Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake.

15 Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu,

16 kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.

17 Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha mu Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu.

18 Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito,

19 mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira kuYerusalemundi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;

20 ndipo chotero ndinachiyesa chinthu chaulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pamalopo Khristu asanatchulidwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.

21 Koma monga kwalembedwa,

Iwo amene uthenga wake sunawafikire, adzaona,

ndipo iwo amene sanamve, adzadziwitsa.

22 Chifukwa chakenso ndinaletsedwa kawirikawiri kudza kwa inu;

23 koma tsopano, pamene ndilibe malo m’maiko akuno, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri kudza kwa inu, ndidzatero,

24 pamene paliponse ndidzapita ku Spaniya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang’ono ndi kukhala ndi inu.

25 Koma tsopano ndipita ku Yerusalemu, ndilikutumikira oyera mtima.

26 Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndiAkayakuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.

27 Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikira iwo ndi zinthu zathupi.

28 Koma pamene ndikatsiriza ichi, ndi kuwasindikizira iwo chipatso ichi, ndidzapyola kwanu kupita ku Spaniya.

29 Ndipo ndidziwa kuti pamene ndikadza kwanu, ndidzafika m’kudzaza kwake kwa chidalitso cha Khristu.

30 Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m’mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine;

31 kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;

32 kuti ndi chimwemwe ndikadze kwa inu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.

33 Ndipo Mulungu wa mtendere akhale ndi inu nonse.Amen.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/15-4aefcb275210cce6597ae577fa691dfb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *