1 Paulo, kapolo wa YesuKhristu,mtumwiwoitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,
2 umene Iye analonjeza kale ndi mau a aneneri ake m’malembo oyera,
3 wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi,
4 amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Khristu Ambuye wathu;
5 amene ife tinalandira naye chisomo ndi utumwi, kuti amvere chikhulupiriro anthu a mitundu yonse chifukwa cha dzina lake;
6 mwa amenewo muli inunso, oitanidwa a Yesu Khristu;
7 kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.
Paulo ayamika Mulungu chifukwa cha chikhulupiriro cha Aroma. Afuna kucheza nao
8 Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.
9 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, mu Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu,
10 ndi kupempha masiku onse m’mapemphero anga, ngati nkutheka tsopano mwa chifuniro cha Mulungu, ndione ulendo wabwino, wakudza kwa inu.
11 Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike;
12 ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa.
13 Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawirikawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthuamitunduena.
Uthenga wake wa Paulo wakuti anthu ayesedwa olungama mwa chikhulupiriro
14 Ine ndili wamangawa wa Agriki ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa.
15 Chotero, momwe ndingakhoze ine, ndilikufuna kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso a ku Roma.
16 Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.
17 Pakuti m’menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.
Kuipitsitsa kwa anthu
18 Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m’chosalungama chao;
19 chifukwa chodziwika cha Mulungu chaonekera m’kati mwao; pakuti Mulungu anachionetsera kwa iwo.
20 Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;
21 chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitire ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamike; koma anakhala opanda pake m’maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira.
22 Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;
23 nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa.
24 Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m’zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi;
25 amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha.Amen.
26 Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwe ao a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe:
27 ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chao wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.
28 Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m’chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;
29 anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;
30 akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,
31 opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo;
32 amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ROM/1-8b6387114411c45a4e1acbb8af72c150.mp3?version_id=1068—