Categories
AMOSI

AMOSI 9

Masomphenya a kulangidwa koopsa

1 Ndinaona Ambuye alikuima paguwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi.

2 Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko.

3 Angakhale abisala pamwamba pa Karimele, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma.

4 Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang’anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai.

5 Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzachita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m’mtsinje; nilidzatsikanso ngati mtsinje wa mu Ejipito;

6 ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m’mwamba, nakhazika tsindwi lake padziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m’nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova.

7 Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israele? Ati Yehova. Sindinakweza Israele ndine, kumtulutsa m’dziko la Ejipito, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?

8 Taonani, maso a Ambuye Yehova ali pa ufumu wochimwawo, ndipo ndidzauononga kuuchotsa padziko lapansi; pokhapo sindidzaononga nyumba ya Yakobo kuitha konse, ati Yehova.

9 Pakuti taonani, ndidzalamulira, ndipo ndidzapeta nyumba ya Israele mwaamitunduonse, monga apeta tirigu m’lichero; koma silidzagwa pansi diso, ndi limodzi lonse.

10 Ochimwa onse a anthu anga adzafa ndi lupanga, ndiwo amene akuti, Choipa sichidzatipeza, kapena kutidulira.

Lonjezo kuti madalitso adzabwera

11 Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;

12 kuti alandire otsala a Edomu akhale cholowa chao, ndi amitundu onse a kutchedwa dzina langa, ati Yehova wakuchita izi.

13 Taonani, akudza masiku, ati Yehova, akuti wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofetsa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka.

14 Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israele, ndipo adzamanganso mizinda ya mabwinja, ndi kukhala m’menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wake, nadzalima minda ndi kudya zipatso zake.

15 Ndipo ndidzawaoka m’dziko mwao ndipo sadzazulidwanso m’dziko lao limene ndawapatsa, ati Yehova Mulungu wako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/AMO/9-b2d22ee4e200fea8de37ea6469b1aa25.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *