Categories
AMOSI

AMOSI 7

Masomphenya atatu, dzombe, moto wonyambita, ndi chingwe cholungamitsa chilili

1 Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa udzu wa chibwereza; ndipo taonani, ndicho chibwereza atawusengera mfumu.

2 Ndipo kunachitika m’mene lidatha kudya msipu wa dziko, ndinati, Ambuye Yehova, khululukiranitu Yakobo; adzakhala chilili bwanji? Popeza ndiye wamng’ono.

3 Ndipo Yehova anachileka. Sichidzachitika, ati Yehova.

4 Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita chakuya chachikulu ukadanyambitanso dziko.

5 Pamenepo ndinati, Ambuye Yehova, lekanitu; Yakobo adzakhala chilili bwanji? Pakuti ali wamng’ono.

6 Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova.

7 Anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangidwa ndi chingwe cholungamitsira chilili; ndi chingwe cholungamitsira chilili m’dzanja lake.

8 Ndipo Yehova anati kwa ine, Amosi, uona chiyani? Ndipo ndinati, Chingwe cholungamitsira chilili. Nati Ambuye, Taona, ndidzaika chingwe cholungamitsira chilili pakati pa anthu anga Israele, sindidzawalekanso:

9 ndi misanje ya Isaki idzakhala bwinja; ndi malo opatulika a Israele adzapasuka; ndipo ndidzaukira nyumba ya Yerobowamu ndi lupanga.

Amosi ndi Amaziya atsutsana ku Betele

10 Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silingathe kulola mau ake onse.

11 Pakuti atero Amosi, Yerobowamu adzafa ndi lupanga, ndi Israele adzatengedwadi ndende, kuchoka m’dziko lake.

12 Amaziya anatinso kwa Amosi, Mlauli iwe, choka, thawira kudziko la Yuda, nudye, nunenere komweko;

13 koma usaneneranso ku Betele; pakuti pamenepo mpamalo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu.

14 Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinalimneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng’ombe, ndi wakutchera nkhuyu;

15 ndipo Yehova ananditenga ndilikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israele.

16 Chifukwa chake tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israele, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isaki;

17 chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m’mzinda, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m’dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m’dziko lake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/AMO/7-861a86eaeb1f9faf748a3a72b42db9e9.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *