Categories
AMOSI

AMOSI 6

Aisraele otsata zilakolako zao adzapsinjika ndi mtundu wina wa anthu

1 Tsoka osalabadirawo muZiyoni, ndi iwo okhazikika m’phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira!

2 Pitani ku Kaline, nimuone; kuchokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? Kapena malire ao aposa malire anu?

3 Inu akutalikitsa tsiku loipa, ndi kusendeza pafupi mpando wachiwawa;

4 ogona pamakama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya anaankhosa a kuzoweta, ndi anaang’ombe ochoka pakati pa khola;

5 akungoimba kutsata maliridwe a zeze, nadzilingiririra zoimbira nazo ngati Davide;

6 akumwera vinyo m’zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe.

7 Chifukwa chake tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.

8 Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zake zachifumu; m’mwemo ndidzapereka mzinda, ndi zonse zili m’menemo.

9 Ndipo kudzachitika, mukatsala amuna khumi m’nyumba imodzi, adzafa.

10 Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m’nyumba, nakati kwa iye ali m’kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova.

11 Pakuti taonani, Yehova walamulira, nadzakantha nyumba yaikulu ichite mpata, ndi nyumba yaing’ono ichite mindala.

12 Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? Kodi adzalimako ndi ng’ombe pakuti mwasanduliza chiweruzo chikhale ndulu, ndi chipatso cha chilungamo chikhale chivumulo;

13 inu okondwera nacho chopanda pake, ndi kuti, Kodi sitinadzilimbitse tokha ndi kulanda Karinaimu mwa mphamvu yathuyathu?

14 Pakuti taonani, ndidzakuutsirani mtundu wa anthu, nyumba ya Israele, ati Yehova Mulungu wa makamu; ndipo adzakupsinjani kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa kuchidikha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/AMO/6-6c5f530b18b73ef358a1f1f30e54dbdd.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *