Aisraele adzadulidwa chifukwa cha zoipa ndi kuuma mtima kwao
1 Tamverani mau awa, inu ng’ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m’phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe.
2 Ambuye Yehova walumbira pali chiyero chake, kuti taonani, adzakugwerani masiku akuti adzakuchotsani ndi zokowera, ndi otsala anu ndi mbedza.
3 Ndipo mudzatulukira popasuka linga, yense m’tsogolo mwake, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.
4 Idzani ku Betele, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m’mawa ndi m’mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatuatatu;
5 nimutenthe nsembe zolemekeza zachotupitsa, nimulalikire nsembe zaufulu, ndi kuzimveketsa; pakuti ichi muchikonda, inu ana a Israele, ati Ambuye Yehova.
6 Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m’mizinda yanu yonse, ndi kusowa mkate m’malo mwanu monse; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
7 Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mzinda umodzi mvula, osavumbitsira mzinda wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m’munda mosavumbidwa mvula munafota.
8 M’mwemo mizinda iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu kumzinda umodzi kukamwa madzi, koma sanakhute; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
9 Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi yaazitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
10 Ndinatumiza mliri pakati panu monga mu Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
11 Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.
12 Chifukwa chake ndidzatero nawe, Israele; popeza ndidzakuchitira ichi, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israele.
13 Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m’mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/AMO/4-c5207feb45d7b96320d57bf4c91c32fd.mp3?version_id=1068—