Categories
AMOSI

AMOSI 2

1 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Mowabu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu asanduke njereza;

2 koma ndidzatumiza moto pa Mowabu, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Keriyoti; ndipo Mowabu adzafa ndi phokoso, ndi kufuula, ndi mau a lipenga;

3 ndipo ndidzalikha woweruza pakati pake, ndi kupha akalonga ake onse, ati Yehova.

Chilango cha Mulungu pa Yuda ndi Israele

4 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Yuda, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza akaniza chilamulo cha Yehova, osasunga malemba ake; ndipo awalakwitsa mabodza ao amene makolo ao anawatsata;

5 koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za muYerusalemu.

6 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Israele, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa chifukwa cha nsapato;

7 ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;

8 nagona pansi pa zofunda za chikole kumaguwa a nsembe ali onse, ndi m’nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.

9 Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m’mwamba, ndi mizu yao pansi.

10 Ndipo ndinakukwezani kuchokera m’dziko la Ejipito, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m’chipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale cholowa chanu.

11 Ndipo ndinaukitsa mwa ana anu aneneri, ndi mwa anyamata anu Anaziri. Si momwemo, inu ana a Israele, ati Yehova?

12 Koma munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera.

13 Taonani, ndidzakupsinjani m’malo mwanu, monga lipsinja galeta lodzala ndi mitolo fwaa.

14 Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;

15 ndi wokoka uta sadzalimbika, ndi waliwiro sadzadzipulumutsa; ngakhale woyenda pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake;

16 ndi wolimba mtima mwa ngwazi adzathawa wamaliseche tsiku lomwelo, ati Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/AMO/2-e43a2d5ebcca96c698a20579f20721a7.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *