Chilango cha Mulungu pa amitundu ozinga Israele
1 Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng’ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.
2 Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali muZiyoni, nadzamveketsa mau ake ali muYerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma.
3 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira zachitsulo;
4 koma ndidzatumiza moto kunyumba ya Hazaele, ndipo udzanyeketsa nyumba zachifumu za Benihadadi.
5 Ndipo ndidzathyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m’chigwa cha Aveni, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova.
6 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Gaza, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatenga ndende anthu onse kuwapereka kwa Edomu;
7 koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zake zachifumu;
8 ndipo ndidzalikha okhala mu Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.
9 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale;
10 koma ndidzatumiza moto pa linga la Tiro, ndipo udzanyeketsa nyumba zake zachifumu.
11 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang’amba ching’ambire nasunga mkwiyo wake chisungire;
12 koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Bozira.
13 Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m’pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao;
14 koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zachifumu zake, ndi kufuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kamvulumvulu;
15 ndipo mfumu yao idzalowa kundende, iyo ndi akalonga ake pamodzi, ati Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/AMO/1-e3e1be81b1dade46fd35afdd8b965bd2.mp3?version_id=1068—