Mau Oyamba
Kolose unali mzinda wina wa ku Asiya, kuvuma kwa Efeso. Paulo si amene adayambitsa mpingo kumeneko, komabe amausamala, poti adatuma anthu ake ku Koloseko kuchokera ku Efeso. Paulo anamva kuti aphunzitsi ena onyenga akusokoneza mpingo umenewo; iwo akuti ofuna kumdziwa Mulungu ndi kupulumuka ayenera kupembedza mafumu ndi akuluakulu akumwamba, ayeneranso kuumbalidwa ndi kutsata miyambo ndi malamulo ena okhudza zakudya ndi zina zotere.
Tsono Paulo awalembera kalatayi kuti atsutse zabodzazi pofotokoza uthenga weniweni wa Chikhristu, makamaka izi zakuti Yesu Khristu yekha ali ndi mphamvu zopulumutsira anthu, koma zimene amalalika aphunzitsi aja zimangosokoneza anthu ndi kuwalekanitsa ndi Khristu. Mulungutu adalenga zinthu zonse kudzera mwa Khristu ndipo amabwezera zonsezo kwa Iye mwini wake kudzera mwa Khristu yemweyo. Anthu a padziko lonse lapansi angayembekeze kupulumuka pokhapo atakhala mwa Khristu ndi kumaphatikana naye. Zotsatira zake nzakuti iwowo aongolere moyo wao potsata zomwe iye Paulo akuwaphunzitsazi.
Potuma Titiko ku Filipi kuti akapereke kalatayi, Paulo atumanso mnyamata wina womperekeza, dzina lake Onesimo; ameneyu ndiye kapolo uja amene nkhani yake ipezeka m’kalata yomwe Paulo adalembera Filemoni.
Za mkatimu
Mau oyamba 1.1-8
Za makhalidwe ndi ntchito za Khristu 1.9—2.19
Za moyo watsopano wokhala mwa Khristu 2.20—4.6
Mau otsiriza 4.7-18