Categories
AKOLOSE

AKOLOSE 4

1 Ambuye inu, chitirani akapolo anu cholungama ndi cholingana; podziwa kuti inunso muli naye Mbuye mu Mwamba.

Awachenjeza za kupemphera ndi za kukhala nayo nzeru

2 Chitani khama m’kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko;

3 ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi chaKhristu; chimenenso ndikhalira m’ndende,

4 kuti ndichionetse ichi monga ndiyenera kulankhula.

5 Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.

6 Mau anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.

Atumidwa Tikiko ndi Onesimo

7 Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tikiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye:

8 amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichi chomwe, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu;

9 pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali wa kwa inu. Zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu.

Malonje

10 Aristariko wam’ndende mnzanga akupatsani moni, ndi Marko, msuweni wa Barnabasi (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),

11 ndi Yesu, wotchedwa Yusto, ndiwo amdulidwe; iwo okha ndiwo antchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.

12 Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbika m’mapemphero ake masiku onse chifukwa cha inu, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m’chifuniro chonse cha Mulungu.

13 Pakuti ndimchitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo ntchito chifukwa cha inu, ndi iwo a mu Laodikea, ndi iwo a mu Hierapoli.

14 Akupatsani moni Luka sing’anga wokondedwa, ndi Dema.

15 Perekani moni kwa abalewo a mu Laodikea, ndi Nimfa, ndiMpingowo wa m’nyumba yao.

16 Ndipo pamene mudamwerenga kalata iyi, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikea, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikea.

17 Ndipo nenani kwa Arkipo, Samaliratu utumiki umene udaulandira mwa Ambuye, kuti uukwanitse.

18 Ndipereka moni ndi dzanja langa, kwa ine Paulo. Kumbukirani zomangira zanga. Chisomo chikhale nanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/COL/4-33250c00bc42ae07f64c5c3c2aefad5d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *