Categories
AKOLOSE

AKOLOSE 3

Atsate kuyeramtima, ndi chikondano cha pa abale

1 Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndiKhristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu.

2 Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

3 Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

4 Pamene Khristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi Iye mu ulemerero.

5 Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;

6 chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;

7 zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m’menemo.

8 Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m’kamwa mwanu:

9 musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,

10 ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye;

11 pamene palibe Mgriki ndi Ayuda,mdulidwendi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m’zonse.

12 Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;

13 kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

14 koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.

15 Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m’mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m’thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.

16 Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.

17 Ndipo chilichonse mukachichita m’mau kapena muntchito, chitani zonse m’dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.

Za banja la munthu

18 Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.

19 Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.

20 Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.

21 Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.

22 Akapolo inu, mverani m’zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye;

23 chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;

24 podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.

25 Pakuti iye wakuchita chosalungama adzalandiranso chosalungama anachitacho; ndipo palibe tsankho.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/COL/3-30da9d2e9a6fcfff941d7b5f91ccc5c6.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *