Categories
AHEBRI

AHEBRI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mlembi wa

Kalata yolembera kwa Ahebri

akufuna kuwalimbitsa mtima Akhristu ena okhala pakati pa anthu ena amene amawavutitsa, kuti asafooke pa chikhulupiriro chao, kuwopa kuti angasiye Chikhristu. Awaonetsa kuti chikhulupiriro choona maziko ake ndi Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, Wansembe wamuyaya, amene apulumutsa omkhulupirira pakuwayanjanitsa ndi Mulungu.

Iye yekha pokhala Mkulu wa ansembe atha kupulumutsa anthu okhulupirira kumachimo, mantha ndi imfa; nsembe zakale zija zinkangofanizira nsembe yeniyeni yomwe Yesu adaipereka pakufera anthu onse.

Mau aakulu mu buku limeneli ali pa 5.8-9 pamene akunena za Yesu kuti, “angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo; ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha.”

Pa mutu 11 iye akupereka zitsanzo za chikhulupiriro cha Aisraele ena otchuka, ndipo akuwauza awerengi ake kuti akhalebe okhulupirika. Pa mutu 12, akuwauzanso kuti akhalebe wokhulupirika mpaka mapeto, nakhazike maso ao pa Yesu, ndi kupirira pamene akumana ndi mazunzo kapena masautso. Bukuli likumaliza ndi malangizo komanso machenjezo.

Za mkatimu

Mulungu adziwululira chonse kudzera mwa Khristu 1.1-3

Za ukulu wake wa Khristu, Mwana wa Mulungu 1.4—4.13

Aposa angelo 1.4-14

Khristu mtsogoleri wa chipulumutso 2.1-18

Aposa Mose yemwe 3.1—4.13

Za ukulu wa unsembe wa Khristu 4.14—10.39

Unsembe wake ndi wamuyaya, apambana Melkizedeki 4.14—7.28

Ukulu wa chipangano chake 8.1—9.28

Ukulu wa nsembe yake 10.1-38

Za chikhulupiriro cha anthu ake 11.1-40

Za chitsanzo cha Yesu Khristu 12.1-29

Mau otsiriza: za m’mene tingakondweretsere Mulungu 13.1-25

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *