Categories
AHEBRI

AHEBRI 11

Za Okhulupirira a mu Chipangano Chakale

1 Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.

2 Pakuti momwemo akulu anachitidwa umboni.

3 Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m’mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwe kuchokera mu zoonekazo.

4 Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.

5 Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeke, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;

6 koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.

7 Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.

8 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.

9 Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m’mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;

10 pakuti analindirira mzinda wokhala nao maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.

11 Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;

12 mwa ichinso kudachokera kwa mmodzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji ngati nyenyezi za m’mwamba, ndi ngati mchenga, uli m’mphepete mwa nyanja, osawerengeka.

13 Iwo onse adamwalira m’chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.

14 Pakuti iwo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao.

15 Ndipotu akadakumbukira lijalo adatulukamo akadaona njira yakubwerera nayo.

16 Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la mu Mwamba; mwa ichi Mulungu sachita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mzinda.

17 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isaki, ndipo iye mene adalandira malonjezano anapereka mwana wake wayekha;

18 amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isaki mbeu yako idzaitanidwa:

19 poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso.

20 Ndi chikhulupiriro Isaki anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zilinkudza.

21 Ndi chikhulupiriro Yakobo, poti alinkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pamutu wa ndodo yake.

22 Ndi chikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, anatchula za matulukidwe a ana a Israele; nalamulira za mafupa ake.

23 Ndi chikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akum’bala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaope chilamuliro cha mfumu.

24 Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi waFarao;

25 nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi;

26 nawerenga tonzo laKhristuchuma choposa zolemera za Aejipito; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphotho.

27 Ndi chikhulupiriro anasiya Ejipito, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.

28 Ndi chikhulupiriro anachitaPaska, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.

29 Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aejipito poyesanso anamizidwa.

30 Ndi chikhulupiriro malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri.

31 Ndi chikhulupiriro Rahabu wadama uja sanaonongeke pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere.

32 Ndipo ndinene chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samisoni, Yefita; za Davide, ndi Samuele ndi aneneri;

33 amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa pa mikango,

34 nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.

35 Akazi analandira akufa ao mwa kuuka kwa akufa; ndipo ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa,

36 kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m’ndende;

37 anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa,

38 (amenewo dziko lapansi silinayenere iwo), osokerera m’mapululu, ndi m’mapiri, ndi m’mapanga, ndi m’mauna a dziko.

39 Ndipo iwo onse adachitidwa umboni mwa chikhulupiriro, sanalandire lonjezanolo,

40 popeza Mulungu adatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe amphumphu opanda ife.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/11-632f7413373adfe690762303cf34f281.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *