1 Pakuti chilamulo, pokhala nao mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.
2 Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbumtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi?
3 Komatu mu izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka.
4 Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.
5 Mwa ichi polowa m’dziko lapansi, anena,
Nsembe ndi chopereka simunazifune,
koma thupi munandikonzera Ine.
6 Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo
simunakondwere nazo;
7 pamenepo ndinati, Taonani, ndafika,
(Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine)
kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.
8 Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifune, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),
9 pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzachita chifuniro chanu. Achotsa choyambacho, kuti akaike chachiwiricho.
10 Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la YesuKhristu, kamodzi, kwatha.
11 Ndipotu wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawirikawiri, zimene sizingathe konse kuchotsa machimo;
12 koma Iye, m’mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala padzanja lamanja la Mulungu chikhalire;
13 kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando kumapazi ake.
14 Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa.
15 Koma Mzimu Woyeranso atichitira umboni; pakuti adatha kunena,
16 Ichi ndichipanganondidzapangana nao,
atapita masiku ajawo, anena Ambuye:
Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao;
ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;
17 ndipo machimo ao ndi kusaweruzika kwao
sindidzakumbukiranso.
18 Koma pomwe pali chikhululukiro cha machimo palibenso chopereka cha kwa uchimo.
Awachenjeza alimbike m’chikhulupiriro
19 Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m’malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,
20 pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake;
21 ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu;
22 tiyandikire ndi mtima woona, m’chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
23 tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
24 ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
25 osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
26 Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo,
27 koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.
28 Munthu wopeputsa chilamulo cha Mose angofa opanda chifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu:
29 ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;
30 pakuti timdziwa Iye amene anati, Kubwezera chilango nkwanga, Ine ndidzabwezera. Ndiponso, Ambuye adzaweruza anthu ake.
31 Kugwa m’manja a Mulungu wamoyo nkoopsa.
32 Koma tadzikumbutsani masiku akale, m’menemo mutaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zowawa;
33 pena pochitidwa chinthu chooneredwa mwa matonzo ndi zisautso; penanso polawana nao iwo ochitidwa zotere.
34 Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m’ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.
35 Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu.
36 Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.
37 Pakuti katsala kanthawi kakang’onong’ono,
ndipo wakudzayo adzafika, wosachedwa.
38 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m’chikhulupiriro:
Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.
39 Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HEB/10-88c37333e42ca597e035e8c20ea5f34e.mp3?version_id=1068—