Categories
AGALATIYA

AGALATIYA 5

Asunge ufulu wa Chikhristu

1 Khristuanatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.

2 Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu.

3 Ndichitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kuchita chilamulo chonse.

4 Mulibe kanthu ndi Khristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo.

5 Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokera m’chikhulupiriro, tilindira chiyembekezo cha chilungamo.

6 Pakuti mwa Khristu Yesu kapenamdulidwekapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.

7 Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi?

8 Kukopa kumene sikuchokera kwa Iye anakuitanani.

9 Chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse.

10 Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakuvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza chitsutso chake.

11 Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo chikhumudwitso cha mtanda chidatha.

12 Mwenzi atadzidula, iwo akugwedezetsani inu.

13 Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.

14 Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

15 Koma ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungaonongane.

Ntchito za thupi ndi zipatso za Mzimu

16 Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.

17 Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.

18 Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.

19 Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa,

20 kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,

21 njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

22 Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

23 chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

24 Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.

25 Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.

26 Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GAL/5-6874a9a58b60e6c51c47ab4708aedf46.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *