Chilamulo sichingathe kupulumutsa; chititsogolera kutifikitsa kwa Khristu
1 Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene YesuKhristuanaonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa?
2 Ichi chokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?
3 Kodi muli opusa otere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mutsiriza ndi thupi?
4 Kodi mudamva zowawa zambiri zotere kwachabe? Ngatitu kwachabe.
5 Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nachita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?
6 Monga Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kunawerengedwa kwa iye chilungamo,
7 chotero zindikirani kuti iwo a chikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu.
8 Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungamaamitundundi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.
9 Kotero kuti iwo a chikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo.
10 Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa,
Wotembereredwa aliyense
wosakhala m’zonse zolembedwa
m’buku la chilamulo, kuzichita izi.
11 Ndipo chidziwikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu; pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro;
12 koma chilamulo sichichokera kuchikhulupiriro; koma, Wakuzichita izi adzakhala ndi moyo ndi izi.
13 Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m’malo mwathu; pakuti kwalembedwa,
Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.
14 Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro.
15 Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo.
16 Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Khristu.
17 Ndipo ichi ndinena: Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lachabe.
18 Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.
19 Nanga chilamulo tsono? Chinaonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndiangelom’dzanja la nkhoswe.
20 Koma nkhoswe siili ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi.
21 Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo.
22 Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.
23 Koma chisanadze chikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira chikhulupiriro chimene chikavumbulutsidwa bwinobwino.
24 Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro.
25 Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi.
26 Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
27 Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.
28 Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.
29 Koma ngati muli a Khristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GAL/3-93bca78fb47160ab321381a8bdc8b7c3.mp3?version_id=1068—