Mau Oyamba
Kalata ya Paulo mtumwi yolembera kwa Aefeso
ikunena za “makonzedwe a Mulungu…ndi makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko”. (1.10) Kalatayi ndi pempho kwa anthu a Mulungu kuti akhale molingana ndi chikonzero chachikuluchi pofuna kuyanjanitsa mtundu wonse wa anthu kudzera mu umodzi umene upezeka mwa Yesu Khristu.
Mu gawo loyamba la buku la
Aefeso
wolembayo akutambasula mutu wa umodzi wa mpingo pamene akukamba za m’mene Mulungu Atate anasankhira anthu ake, ndipo m’mene iwowo amalandira chikhululukiro cha machimo namasulidwa kuchokera kumachimo kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu. Komanso akukamba za lonjezo lalikulu la Mulungu limene litsimikizidwa ndi Mzimu Woyera. Mu gawo lachiwiri iye akuwadandaulira awerengi ake kuti umodzi wao mwa Khristu uwonekere poyera pa mayendedwe ao ndi pa moyo wao wonse.
M’kalatamu akugwiritsa ntchito zifanizo zingapo pofuna kuonetsa umodzi wa anthu a Mulungu mwa Khristu: mpingo uli ngati thupi, ndipo Khristu ali ngati mutu wake; kapenanso ngati nyumba, ndipo Khristu ndiye mwala wokhala pangodya; kapenanso ngati mkazi, ndipo Khristu ndiye mwamuna wake wa mpingo. Kenaka kalatayi ikufotokoza zinthu zinanso zofunikira pamene wolembayo akunena za chisomo cha Mulungu mwa Khristu. Chilichonse chikuyesedwa molingana ndi chikondi, kudzipereka, kukhululukira machimo, chisomo komanso chiyero cha Khristu.
Za mkatimu
Mau oyamba 1.1-2
Khristu ndi mpingo 1.3—3.21
Moyo watsopano mwa Khristu 4.1—6.20
Mau omaliza 6.21-24