Categories
AEFESO

AEFESO 6

1 Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino.

2 Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano),

3 kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.

4 Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.

5 Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukira kanthu kena, monga kwaKhristu;

6 si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima;

7 akuchita ukapolo ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu ai;

8 podziwa kuti chinthu chokoma chilichonse yense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.

9 Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali mu Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye.

Zida za Mulungu

10 Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake.

11 Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.

12 Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m’zakumwamba.

13 Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.

14 Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m’chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo;

15 ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere;

16 koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.

17 Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu;

18 mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,

19 ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m’kunditsegulira m’kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino,

20 chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m’menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.

Tikiko apita naye kalatayo

21 Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye;

22 amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu.

23 Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu.

24 Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m’chosaonongeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EPH/6-ee0a8676fc9c50e57912570a3ac98a73.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *