Categories
2 YOHANE

2 YOHANE 1

1 Mkuluyo kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake, amene ine ndikondana nao m’choonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira choonadi;

2 chifukwa cha choonadi chimene chikhala mwa ife, ndipo chidzakhala ndi ife ku nthawi yosatha:

3 Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa YesuKhristuMwana wa Atate, m’choonadi ndi m’chikondi.

Za chikondano. Za aphunzitsi onyenga

4 Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m’choonadi, monga tinalandira lamulo lochokera kwa Atate.

5 Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tinali nalo kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake.

6 Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo.

7 Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m’dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m’thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.

8 Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.

9 Yense wakupitirira, wosakhala m’chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu; iye wakukhala m’chiphunzitso, iyeyo ali nao Atate ndi Mwana.

10 Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musampatse moni.

11 Pakuti iye wakumpatsa moni ayanjana nazo ntchito zake zoipa.

12 Pokhala ndili nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti chimwemwe chanu chikwanire.

13 Akupereka moni ana a mbale wanu wosankhika.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2JN/1-36bd159537e75f3891bea6c2f03289ff.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *