1 Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m’chisomo cha mwaKhristuYesu.
2 Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.
3 Umve zowawa pamodzi nane monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu.
4 Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.
5 Koma ngatinso wina ayesana nao m’makani amasewero, samveka korona ngati sanayesane monga adapangana.
6 Wam’munda wogwiritsitsa ntchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozo.
7 Lingirira chimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa chidziwitso m’zonse.
8 Kumbukira Yesu Khristu, wouka kwa akufa, wochokera m’mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga;
9 m’menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mau a Mulungu samangika.
10 Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.
11 Okhulupirika mauwa: Pakuti ngati tidamwalira ndi Iye, tidzakhalanso moyo ndi Iye:
12 ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:
13 ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sangathe kudzikana yekha.
Umo azichita ndi osochera
14 Uwakumbutse izi, ndi kuwachitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asachite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.
15 Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.
16 Koma pewa nkhani zopanda pake; pakuti adzapitirira kutsata chisapembedzo,
17 ndipo mau ao adzanyeka chilonda; a iwo ali Himeneo ndi Fileto;
18 ndiwo amene adasokera kunena za choonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwachitika kale, napasula chikhulupiriro cha ena.
19 Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.
20 Koma m’nyumba yaikulu simuli zotengera za golide ndisilivazokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu.
21 Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chopatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino.
22 Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.
23 Koma mafunso opusa ndi opanda malango upewe, podziwa kuti abala ndeu.
24 Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,
25 wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,
26 ndipo akadzipulumutse kumsampha wa mdierekezi, m’mene anagwidwa naye, kuchifuniro chake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2TI/2-f999249bd350206181f893226ccd5431.mp3?version_id=1068—