Nyimbo yoyamikira Yehova ya Davide
1 Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m’dzanja la adani ake onse, ndi m’dzanja la Saulo.
2 Ndipo anati,
Yehova ndiye thanthwe langa,
ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi.
3 Mulungu wa thanthwe langa,
Iye ndidzamkhulupirira;
chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa,
nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga;
Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.
4 Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande;
chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.
5 Pakuti mafunde a imfa anandizinga,
mitsinje ya zopanda pake inandiopsa ine.
6 Zingwe za kumanda zinandizingira;
misampha ya imfa inandifikira ine.
7 M’kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova,
inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga;
ndipo Iye anamva mau anga ali mu Kachisi wake,
ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.
8 Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira.
Maziko a dziko la kumwamba anasunthika.
Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya.
9 M’mphuno mwake munatuluka utsi,
ndi moto wotuluka m’kamwa mwake unaononga;
makala anayaka nao.
10 Anaweramitsa miyambanso, natsika;
ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake.
11 Ndipo Iye anaberekeka pakerubinauluka;
inde anaoneka pa mapiko a mphepo.
12 Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira Iye,
kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yochindikira ya mlengalenga.
13 Cheza cha pamaso pake
makala a moto anayaka.
14 Yehova anagunda kumwamba;
ndipo Wam’mwambamwamba ananena mau ake.
15 Ndipo Iye anatumiza mivi, nawawaza;
mphezi, nawaopsa.
16 Pamenepo m’munsi mwa nyanja munaoneka,
maziko a dziko anaonekera poyera,
ndi mtonzo wa Yehova,
ndi mpumo wa mpweya wa m’mphuno mwake.
17 Iye anatumiza kuchokera kumwamba nanditenga;
Iye ananditulutsa m’madzi aakulu.
18 Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,
kwa iwo akudana ndi ine;
pakuti anandiposa mphamvu.
19 Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;
koma Yehova anali mchirikizo wanga.
20 Iye ananditulutsanso ku malo aakulu;
Iye anandipulumutsa,
chifukwa akondwera ndi ine.
21 Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa;
monga mwa kuyera kwa manja anga anandipatsa mphotho.
22 Pakuti ndinasunga njira za Yehova,
osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga.
23 Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga;
ndipo za malemba ake, sindinawapatukire.
24 Ndinakhalanso wangwiro kwa Iye,
ndipo ndinadzisunga kusachita kuipa kwanga.
25 Chifukwa chake Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa;
monga mwa kuyera kwanga pamaso pake.
26 Ndi chifundo Inu mudzadzionetsa wachifundo,
ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro.
27 Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima;
ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.
28 Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa;
koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse.
29 Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova;
ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.
30 Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu;
ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.
31 Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro;
mau a Yehova anayesedwa;
Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.
32 Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova?
Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?
33 Mulungu ndiye linga langa lamphamvu;
ndipo Iye ayendetsa angwiro mu njira yake.
34 Iye asandutsa mapazi ake akunga mapazi a mbawala;
nandiika pa misanje yanga.
35 Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;
kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.
36 Ndiponso munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu;
ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.
37 Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga,
ndi mapazi anga sanaterereke.
38 Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga;
ndiponso sindinabwerere mpaka nditawatha.
39 Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sangathe kuuka,
inde anagwa pansi pa mapazi anga.
40 Pakuti Inu munandimanga m’chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo;
munandigonjetsera akundiukira.
41 Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,
kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.
42 Anayang’ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;
ngakhale kwa Yehova, koma Iye sanawayankhe.
43 Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati fumbi la padziko,
ndinawapondereza ngati dothi la m’makwalala.
44 Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;
munandisunga ndikhale mutu waamitundu;
Anthu amene sindinawadziwe adzanditumikira ine.
45 Alendo adzandigonjera ine,
pakumva za ine, adzandimvera pomwepo.
46 Alendo adzafota,
nadzabwera ndi kunthunthumira otuluka mokwiririka mwao.
47 Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;
ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la chipulumutso changa;
48 inde Mulungu wakundibwezera chilango ine,
ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.
49 Amene anditulutsa kwa adani anga;
inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira;
mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa.
50 Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu,
ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu.
51 Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu;
naonetsera chifundo wodzozedwa wake,
kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/22-06f0c38dcd56c1f96249c9363cdb4311.mp3?version_id=1068—