Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 18

Abisalomu agonja pankhondo, naphedwa

1 Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.

2 Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang’anire Yowabu, lina aliyang’anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang’anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu.

3 Koma anthuwo anati, Simudzatuluka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; chifukwa chake tsono nkwabwino kuti mutithandize kutuluka m’mzinda.

4 Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzachita chimene chikomera inu. Mfumu inaima pambali pa chipata, ndipo anthu onse anatuluka ali mazana, ndi zikwi.

5 Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.

6 Chomwecho anthuwo anatulukira kuthengo kukamenyana ndi Israele; nalimbana ku nkhalango ya ku Efuremu.

7 Ndipo anthu a Israele anakanthidwa pamenepo pamaso pa anyamata a Davide, ndipo kunali kuwapha kwakukulu kumeneko tsiku lomwelo, anthu zikwi makumi awiri.

8 Pakuti nkhondo inatanda padziko lonse, ndipo tsiku lomwelo nkhalango inaononga anthu akuposa amene anaonongeka ndi lupanga.

9 Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yake, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkulu. Ndipo mutu wake unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye inapitirira.

10 Ndipo munthu wina anamuona, nauza Yowabu, nati, Onani, ndaona Abisalomu ali lende pathundu.

11 Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba.

12 Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m’dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m’kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.

13 Ndikadachita chonyenga pa moyo wake, palibe mlandu ubisika kwa mfumu; ndipo inu nomwe mukadanditsutsa.

14 Pomwepo Yowabu anati, Sindiyenera kuchedwa nawe. Natenga mikondo itatu nagwaza nayo mtima wa Abisalomu alikukhala wamoyo pakati pa mtengowo.

15 Ndipo anyamata khumi onyamula zida zake za Yowabu anamzungulira Abisalomu namkantha namupha.

16 Ndipo Yowabu analiza lipenga, ndipo anthu anabwerera naleka kupirikitsa Aisraele; pakuti Yowabu analetsa anthuwo.

17 Ndipo anatenga Abisalomu namponya m’chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake.

18 Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira choimiritsacho chili m’chigwa cha mfumu; pakuti anati, Ndilibe mwana wamwamuna adzakhala chikumbutso cha dzina langa; natcha choimiritsacho ndi dzina la iye yekha; ndipo chitchedwa chikumbutso cha Abisalomu, kufikira lero lomwe.

Davide alira Abisalomu

19 Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera chilango adani ake.

20 Ndipo Yowabu ananena naye, Sudzakhala iwe wotengera mau lero, koma tsiku lina udzatengera mau; koma lero sudzatengera mau, chifukwa mwana wa mfumu wafa.

21 Pamenepo Yowabu ananena ndi Mkusi, Kauze mfumu zimene unaziona. Ndipo Mkusi anawerama kwa Yowabu, nathamanga.

22 Ndipo Ahimaazi mwana wa Zadoki ananena kachiwiri kwa Yowabu, Komatu, mundilole ndithamange inenso kutsata Mkusi. Ndipo Yowabu anati, Udzathamangiranji, mwana wanga, popeza sudzalandira mphotho ya pa mauwo?

23 Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange. Iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kuchigwa, napitirira Mkusi.

24 Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.

25 Pamenepo mlondayo anafuula, nauza mfumu. Mfumuyo niti, Ngati ali yekha alikubwera ndi mau. Ndipo iye uja anayenda msanga, nayandikira.

26 Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakuchipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, Iyenso abwera ndi mau.

27 Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki. Ndipo mfumu inati, Iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma.

28 Ndipo Ahimaazi anafuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yake pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.

29 Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yowabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringupiringu, koma sindinadziwe ngati kutani.

30 Ndipo mfumu inati, Patuka nuime apa. Napatuka, naimapo.

31 Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu.

32 Ndipo mfumu inanena ndi Mkusiyo, Mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Mkusiyo nayankha, Adani a mbuye wanga mfumu, ndi onse akuukira inu kukuchitirani zoipa, akhale monga mnyamata ujayo.

33 Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/18-f350444df31a95afcb7a1577118c8f26.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *