1 Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide;
2 ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;
3 ndipo anthu onsewo ndidzabwera nao kwa inu; munthu mumfunayo ali ngati onse obwerera; momwemo anthu onse adzakhala mumtendere.
4 Ndipo mauwa anamuyenerera Abisalomu, ndi akulu onse a Israele.
Uphungu wa Husai
5 Pomwepo Abisalomu anati, Kaitane tsopano Husai Mwariki yemwe, timvenso chimene anene iye.
6 Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofele analankhula mau akuti; tichite kodi monga mwa kunena kwake? Ngati iai, unene ndiwe.
7 Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofele suli wabwino.
8 Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ake kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga chimbalangondo chochilanda ana ake kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.
9 Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, aliyense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu.
10 Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wake ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisraele onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi.
11 Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake.
12 Chomwecho tidzamvumbulukira pamalo akuti adzapezeka, ndipo tidzamgwera monga mame agwa panthaka, ndipo sitidzasiya ndi mmodzi yense wa iye ndi anthu onse ali naye.
13 Ndiponso ngati walowa kumzinda wina, Aisraele onse adzabwera ndi zingwe kumzindako, ndipo tidzaukokera kumtsinje, kufikira sikapezeka kamwala kakang’ono kumeneko.
14 Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.
15 Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, Ahitofele anapangira Abisalomu ndi akulu a Israele zakutizakuti; koma ine ndinapangira zakutizakuti.
16 Chifukwa chake tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti Musagona usiku uno pa madooko a kuchipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.
17 Ndipo Yonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogele; mdzakazi ankapita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m’mzinda.
18 Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anachoka msanga onse awiri, nafika kunyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali nacho chitsime pabwalo pake; ndipo anatsikira m’menemo.
19 Ndipo mkazi anatenga chivundikiro nachiika pakamwa pa chitsime, napapasapo lipande la tirigu; momwemo sichinadziwike.
20 Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka kuYerusalemu.
Davide ndi anthu ake aoloka Yordani
21 Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anatuluka m’chitsime, nanka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofele anapangira zotere pa inu.
22 Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordani. Kutacha m’mawa sanasowe mmodzi wa iwo wosaoloka Yordani.
23 Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m’manda a atate wake.
Abisalomu ndi anthu ake aolokanso Yordani
24 Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordani, iye ndi anthu onse a Israele pamodzi naye.
25 Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m’malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.
26 Ndipo Israele ndi Abisalomu anamanga zithando m’dziko la Giliyadi.
27 Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,
28 iwo anabwera nao makama, ndi mbale, ndi zotengera zadothi, ndi tirigu, ndi barele, ndi ufa, ndi tirigu wokazinga, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi zokazinga zina,
29 ndi uchi ndi mafuta, ndi nkhosa, ndi mase a ng’ombe, kuti adye Davide, ndi anthu amene anali naye; pakuti anati, Anthu ali ndi njala, olema, ndi aludzu m’chipululumo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/17-f2adeb6b8e61aada20305195d2310c17.mp3?version_id=1068—