Tchimo loopsa la Aminoni
1 Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye.
2 Ndipo Aminoni anapsinjikadi nayamba kudwala chifukwa cha mlongo wake Tamara, pakuti anali namwali, ndipo Aminoni anachiyesa chapatali kumchitira kanthu.
3 Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake ndiye Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide. Ndipo Yonadabu anali munthu wochenjera ndithu.
4 Nanena naye, Iwe mwana wa mfumu, uonderanji tsiku ndi tsiku? Sungandiuze kodi? Ndipo Aminoni anati kwa iye, Ndikonda Tamara, mlongo wa mbale wanga Abisalomu.
5 Ndipo Yonadabu ananena naye, Ugone pa kama wako ndi kudzikokomera ulikudwala; ndipo pamene atate wako akadzakuona unene naye, Mulole mlongo wanga Tamara abwere kundipatsa kudya, nakonzere chakudyacho pamaso panga kuti ndichione ndi kuchidya cha m’manja mwake.
6 Chomwecho Aminoni anagona, nadzikokomeza alikudwala; ndipo pamene mfumu inadza kumuona, Aminoni anati kwa mfumuyo, Mulole Tamara mlongo wanga abwere ndi kundipangira timitanda tiwiri pamaso panga, kuti ndikadye cha m’manja mwake.
7 Ndipo Davide anatumiza mau kwao kwa Tamara, kuti, Upite kunyumba ya mlongo wako Aminoni, numkonzere chakudya.
8 Chomwecho Tamara anapita kunyumba ya mlongo wake Aminoni; ndipo iye anali chigonere. Ndipo anatenga ufa naukanda naumba timitanda pamaso pake, nakazinga timitandato.
9 Ndipo anatenga chiwaya natitulutsa pamaso pake; koma anakana kudya. Ndipo Aminoni anati, Anthu onse atuluke kundisiya ine. Natuluka onse, kumsiya.
10 Ndipo Aminoni anati kwa Tamara, Bwera nacho chakudya kuchipinda kuti ndikadye cha m’manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kuchipinda kwa Aminoni mlongo wake.
11 Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga.
12 Koma iye anamyankha nati, Iai, mlongo wanga, usandichepetsa ine, pakuti chinthu chotere sichiyenera kuchitika mu Israele, usachita kupusa kumeneku.
13 Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? Ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru mu Israele. Chifukwa chake tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine.
14 Koma iye sadafune kumvera mau ake, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkakamiza, nagona naye.
15 Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka.
16 Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti choipa ichi chakuti ulikundipirikitsa nchachikulu choposa china chija unandichitira ine. Koma anakana kumvera.
17 Pomwepo anaitana mnyamata wake amene anamtumikira, nati, Tulutsa mkazi uyu kwa ine, nupiringidze chitseko atapita iye.
18 Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana aakazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye.
19 Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pake, nang’amba chovala cha mawangamawanga chimene analikuvala, nagwira dzanja lake pamutu pake, namuka nayenda, nalira komveka.
20 Ndipo Abisalomu mlongo wake ananena naye, Kodi mlongo wako Aminoni anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale chete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usavutika ndi chinthuchi. Chomwecho Tamara anakhala wounguluma m’nyumba ya Abisalomu mlongo wake.
21 Koma pamene mfumu Davide anamva zonsezi, anakwiya ndithu.
22 Ndipo Abisalomu sanalankhule ndi Aminoni chabwino kapena choipa, pakuti Abisalomu anamuda Aminoni popeza adachepetsa mlongo wake Tamara.
23 Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana aamuna onse a mfumu.
24 Abisalomu nafika kwa mfumu nati, Onani, ine mnyamata wanu ndili nao osenga nkhosa; inu mfumu ndi anyamata anu mupite nane mnyamata wanu.
25 Ndipo mfumu inati kwa Abisalomu, Iai mwana wanga, tisapite tonse, kuti tingakuchulukire. Ndipo iye anaiumirira koma inakana kupita; koma inamdalitsa.
26 Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Aminoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, Iye apitirenji nawe?
27 Koma Abisalomu anaiumirira iyo, nilola kuti Aminoni ndi ana aamuna onse a mfumu apite naye.
28 Ndipo Abisalomu analamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna.
29 Ndipo anyamata a Abisalomu anamchitira Aminoni monga umo Abisalomu anawalamulira. Pomwepo ana aamuna onse a mfumu ananyamuka, nakwera munthu yense pa nyuru yake, nathawa.
30 Ndipo kunali akali panjira, mau anafika kwa Davide, kuti, Abisalomu anapha ana aamuna onse a mfumu, osatsalapo ndi mmodzi yense.
31 Pamenepo mfumu inanyamuka ning’amba zovala zake nigona pansi, ndipo anyamata ake onse anaimirirapo ndi zovala zao zong’ambika.
32 Ndipo Yonadabu mwana wa Simea mbale wa Davide anayankha nati, Mbuye wanga asaganize kuti anapha anyamata onse, ana aamuna a mfumu, pakuti Aminoni yekha wafa, pakuti ichi chinatsimikizika ndi mau a Abisalomu kuyambira tsiku lija anachepetsa mlongo wake Tamara.
33 Chifukwa chake tsono mfumu mbuye wanga asasauke mtima ndi chinthuchi, ndi kuganiza kuti ana aamuna onse a mfumu afa; pakuti Aminoni yekha wafa.
34 Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang’ana, ndipo onani, m’mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m’njira yolambalala phiri.
35 Ndipo Yonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana aamuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo.
36 Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana aamuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ake analira ndi kulira kwakukulu ndithu.
37 Koma Abisalomu anathawa, nanka kwa Talimai mwana wa Amihudi mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide analira mwana wake tsiku ndi tsiku.
38 Chomwecho anathawa Abisalomu, nanka ku Gesuri, nakakhala kumeneko zaka zitatu.
39 Ndipo mfumu Davide analira kunka kwa Abisalomu, chifukwa anasangalatsidwa pa imfa ya Aminoni.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/13-5408388322be30f7da06a807c7b58033.mp3?version_id=1068—