Kulapa ndi kulangidwa kwa Davide
1 Ndipo Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Ndipo anafika kwa iye nanena naye, Mu mzinda wina munali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka.
2 Wolemerayo anali nazo zoweta zazing’ono ndi zazikulu zambiri ndithu;
3 koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kanadyako chakudya chake cha iye yekha, kanamwera m’chikho cha iye yekha, kanagona pa chifukato chake, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wake wamkazi.
4 Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zake zazing’ono ndi zazikulu, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatengamwanawankhosawa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye.
5 Pamenepo mkwiyo wa Davide unayaka ndithu pa munthuyo, nati kwa Natani, Pali Yehova, munthu amene anachita ichi, ayenera kumupha;
6 ndipo adzabwezera mwa mwanawankhosayo ena anai, chifukwa anachita ichi osakhala nacho chifundo.
7 Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupulumutsa m’dzanja la Saulo;
8 ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako, ndi akazi a mbuye wako pa chifukato chako, ndinakupatsanso nyumba ya Israele ndi ya Yuda; ndipo zimenezi zikadakuchepera ndikadakuonjezera zina zakutizakuti.
9 Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.
10 Chifukwa chake tsono lupanga silidzachoka pa nyumba yako nthawi zonse, popeza unandipeputsa Ine, nudzitengera mkazi wa Uriya Muhiti akhale mkazi wako.
11 Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m’nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene.
12 Pakuti iwe unachichita m’tseri; koma Ine ndidzachita chinthu ichi pamaso pa Aisraele onse, dzuwa lili nde.
13 Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.
14 Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.
15 Ndipo Natani anamuka kwao. Ndipo Yehova anadwaza mwana amene mkazi wa Uriya anambalira Davide, nadwala kwambiri.
16 Chifukwa chake Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.
17 Ndipo akulu a m’nyumba yake ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.
18 Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwanji kuti mwana wafa; sadzadzichitira choipa nanga?
19 Koma pamene Davide anaona anyamata ake likunong’onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ake, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa.
20 Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye.
21 Pamenepo anyamata ake ananena naye, Ichi mwachita nchiyani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya.
22 Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandichitira chifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo.
23 Koma tsopano wafa, ndidzasaliranjinso kudya? Kodi ndikhoza kumbweza? Ine ndidzamuka kuli iye, koma iye sadzabweranso kwa ine.
Kubadwa kwa Solomoni
24 Ndipo Davide anasangalatsa Bateseba mkazi wake, nalowa kwa iye, nagona naye; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Solomoni. Ndipo Yehova anamkonda iye,
25 natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova.
26 Ndipo Yowabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mzinda wachifumu.
27 Yowabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mzinda wa pamadzi.
28 Chifukwa chake tsono musonkhanitse anthu otsalawo, nimumangire mzindawo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mzindawo, ndipo ungatchedwe ndi dzina langa.
29 Ndipo Davide anasonkhanitsa anthu onse, napita ku Raba, naponyana nao, naulanda.
30 Nachotsa korona pamutu wa mfumu yao; kulemera kwake kunali talente wa golide; ndipo m’menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pamutu wa Davide. Iye natulutsa zofunkha za mzindawo zambirimbiri.
31 Natulutsa anthu a m’mzindamo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi nkhwangwa zachitsulo; nawapsitiriza ndi chitsulo, nawapititsa m’ng’anjo yanjerwa; natero ndi mizinda yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kunka kuYerusalemu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/12-60921e5225c98717730cd496a982e5aa.mp3?version_id=1068—