Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 1

Amuuza Davide za imfa ya Saulo

1 Ndipo kunali atamwalira Saulo, pamene Davide anabwera atawapha Aamaleke, ndipo Davide atakhala ku Zikilagi masiku awiri;

2 pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong’ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.

3 Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? Iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israele.

4 Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? Undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Saulo ndi Yonatani mwana wake anafanso.

5 Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani mwana wake anafa?

6 Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda paphiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza.

7 Ndipo iye pakucheukira m’mbuyo mwake anandiona, nandiitana. Ndipo ndinayankha, Ndine.

8 Nanena, Ndiwe yani? Ndipo ndinayankha kuti, Ndine Mwamaleke.

9 Ndipo anati kwa ine, Uime pa ine nundiphe, chifukwa kuwawa mtima kwandigwera ine, popeza ndikali moyobe.

10 M’mwemo ndinakhala pambali pake ndi kumtsiriza chifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wake, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pake, ndi chigwinjiri cha pa mkono wake, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga.

11 Pomwepo Davide anagwira zovala zake nazing’amba; nateronso anthu onse okhala naye.

12 Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.

13 Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuzayo, Kwanu nkuti? Nayankha, Ine ndine mwana wa mlendo, Mwamaleke.

14 Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaope kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova?

15 Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe. Ndipo anamkantha, nafa iye.

16 Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; chifukwa pakamwa pako padachita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova.

Davide alirira Saulo ndi Yonatani

17 Ndipo Davide analirira Saulo ndi Yonatani mwana wake ndi nyimbo iyi ya maliro;

18 nawauza aphunzitse ana Ayuda nyimbo iyi ya Uta, onani inalembedwa m’buku la Yasara,

19 Ulemerero wako, Israele, unaphedwa pa misanje yako.

Ha! Adagwa amphamvu!

20 Usachinene ku Gati,

usachibukitse m’makwalala a Asikeloni,

kuti ana aakazi a Afilisti angasekere,

kuti ana aakazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.

21 Mapiri inu a Gilibowa,

pa inu pasakhale mame kapena mvula,

kapena minda yakutengako zopereka.

Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa,

chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.

22 Uta wa Yonatani sunabwerere,

ndipo lupanga la Saulo silinabwerere chabe,

pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.

23 Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m’miyoyo yao,

ndipo mu imfa yao sanasiyane;

anali nalo liwiro loposa chiombankhanga,

anali amphamvu koposa mikango.

24 Ana aakazi inu a Israele, mulirire Saulo,

amene anakuvekani ndi zofiira zokometsetsa,

amene anaika zokometsetsa zagolide pa zovala zanu.

25 Ha! Amphamvuwo anagwa pakati pa nkhondo!

Yonatani anaphedwa pamisanje pako.

26 Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe,

mbale wanga Yonatani;

wandikomera kwambiri;

chikondi chako, ndinadabwa nacho,

chinaposa chikondi cha anthu aakazi.

27 Ha! Amphamvuwo anagwa,

ndi zida za nkhondo zinaonongeka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/1-1c93e06fecc8f07e74cfd9f28faf5269.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *